1Ndimakonda Chauta
chifukwa amamva mau anga omupemba.
2Iye amatchera khutu kuti andimve,
nchifukwa chake ndidzampempha
nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
3Misampha ya imfa idandizinga,
zoopsa za m'dziko la akufa zidandigwera.
Ndidaona mavuto, nkugwidwa ndi nthumanzi.
4Tsono ndidapemphera potchula dzina la Chauta kuti,
“Chauta ndikukupemphani, pulumutsani moyo wanga.”
5Chauta ndi wokoma mtima ndi wolungama.
Mulungu wathu ndi wachifundo.
6Chauta amasunga a mtima wodzichepetsa.
Pamene ndidagwa m'zoopsa, Iye adandipulumutsa.
7Iwe mtima wanga, bwerera ku malo ako opumulira,
chifukwa Chauta wakuchitira zokoma.
8Pakuti Inu Chauta, mwandipulumutsa ku imfa,
mwaletsa misozi yanga,
mwanditeteza kuti ndisaphunthwe.
9Ndimayenda pamaso pa Chauta
m'dziko la amoyo.
10 2Ako. 4.13 Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati,
“Ndazunzika koopsa.”
11Pamene ndinkachita mantha, ndidati,
“Anthu ndi osakhulupirika.”
12Ndidzambwezera chiyani Chauta
pa zabwino zonse zimene adandichitira?
13Ndidzakweza chikho cha chipulumutso,
ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
14Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta
pamaso pa anthu ake onse.
15Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta,
ndi yamtengowapatali pamaso pake.
16Chauta, ine ndine mtumiki wanu,
mtumiki wanu weniweni,
mwana wa mdzakazi wanu.
Inu mwamasula maunyolo anga.
17Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera,
ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
18Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta
pamaso pa anthu ake onse.
19Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu,
mu mzinda wa Yerusalemu.
Tamandani Chauta!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.