Akol. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu.

2Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu.

Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

Paulo ayamika Mulungu chifukwa cha akhristu a ku Kolose

3Tikamakupemphererani, nthaŵi zonse timathokoza Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.

4Timathokoza chifukwa tamva kuti mumakhulupirira Khristu Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu onse a Mulungu.

5Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino.

6Uthenga Wabwinowu ukubala zipatso ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi, monga momwe wachitiranso pakati panu, kuyambira tsiku limene mudamva ndi kumvetsa za kukoma mtima kwa Mulungu.

7Akol. 4.12; Fil. 1.23Mudaphunzira zimenezi kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa. Iye uja akugwirira ntchito Khristu mokhulupirika m'malo mwathu.

8Ndiye amene adatidziŵitsa za chikondi chomwe Mzimu Woyera adaika mwa inu.

Paulo apempherera akhristu a ku Kolose

9Nchifukwa chake, kuyambira tsiku limene tidamva zimenezi, sitileka kukupemphererani. Timapempha Mulungu kuti akudzazeni ndi nzeru ndi luntha, zimene Mzimu Woyera amapatsa, kuti mumvetse zonse zimene Iye afuna.

10Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.

11Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yaulemerero, kuti muzipirira zonse ndi mitima yoleza ndi yosangalala.

12Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala.

13Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.

14Aef. 1.7Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Za makhalidwe ndi ntchito za Khristu

15 Lun. 7.26 Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka.

Iye ndiye Mwana wake woyamba,

wolamulira zolengedwa zonse.

16Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse

zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka,

mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse.

Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye,

zonsezo adalengera Iyeyo.

17Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe,

mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.

18 Aef. 1.22, 23 Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake.

Ndiye chiyambi chake,

Woyambirira mwa ouka kwa akufa,

kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu.

19Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse

ukhalemo mwa Khristuyo.

20 Aef. 2.16 Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso

zinthu zonse ndi Iye mwini,

zapansipano ndi za Kumwamba.

Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere

kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.

21Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa.

22Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.

23Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.

Za m'mene Paulo akutumikira mpingo

24Tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zoŵaŵazo, ndikutsiriza m'thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo.

25Ndipo ine ndine mtumiki wa Mpingowu, pakuti Mulungu ndiye adandipatsa ntchitoyi yoti ndikulalikireni kwathunthu mau ake.

26Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake.

27Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero.

28Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

29Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help