1Padapita nthaŵi yaikulu chiyambire pamene Chauta adakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraele ndi adani ao oŵazungulira. Pamenepo nkuti Yoswa atatheratu nkukalamba.
2Tsono Yoswayo adaitana Aisraele onse, pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a anthuwo, naŵauza kuti “Tsopano ine ndakalamba.
3Zonse zimene Chauta wachitira mitundu ina yonseyi chifukwa cha inu, mwazipenya. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene wakumenyerani nkhondo.
4Tamvani tsono, mitundu imene simudaipambanebe, ndaipereka kwa mafuko anu, chimodzimodzi mitundu inayo imene ndidaiwononga pakati pa Yordani ndi Nyanja Yaikulu kuzambweko.
5Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaŵathaŵitse pamaso panu. Inuyo mudzatenga maiko ao monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakulonjezerani.
6Motero, muchenjere kuti mumvere ndi kumachitadi zonse zomwe zidalembedwa m'buku la malamulo a Mose. Musanyozere gawo lina lililonse la malamulowo,
7ndipo musagwirizane ndi anthu aŵa amene atsala pakati panu. Musamatchula maina a milungu yao kapena kulumbira poitchula, kapena kumaitumikira, kapenanso kumaigwadira.
8Mukamakhulupirira Chauta, monga momwe mwachitira mpaka tsopano lino,
9Chauta adzakupirikitsirani mitundu yaikuluikulu ndi yamphamvu. Mpaka pano, palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulimbana nanu.
10Deut. 32.30; Deut. 3.22 Aliyense mwa inu angathe kuthamangitsa anthu chikwi chimodzi, chifukwa Chauta ndiye akukumenyerani nkhondo monga adalonjezera.
11Musamale kwambiri tsono kuti mukonde Chauta, Mulungu wanu.
12Mukabwerera m'mbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalira ili pakati panuyi, ndi kumakwatirana nayo,
13pamenepo mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu. Koma anthuwo adzakhala ngati msampha kwa inu, kapenanso ngati khwekhwe. Adzakhalanso ngati chikoti choŵaŵa pamsana panu, kapena ngati minga zokulasani m'maso mwanu. Zimenezi zidzachitikabe mpaka inuyo mutatha m'dziko labwinoli limene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani.
14“Ine ndi ulendo uno tsopano. Aliyense mwa inu akudziŵa bwino lomwe mumtima mwake ndi mumzimu mwake kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza. Zonse zimene adaalonjeza, zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silidachitike.
15Monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani zabwino zonse zimene adaanena kuti adzachita, choncho angathe kukuchitani zoipa, mpaka kukuchotsani m'dziko lokomali limene Iye adakupatsani.
16Ngati simusunga chipangano chomwe Chauta adakulamulani, mukamapita kukatumikira milungu ina ndi kumakaigwadira, Chauta adzakupserani mtima, ndipo sipadzatsala ndi mmodzi yense m'dziko labwino limene adakupatsanilo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.