Oba. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kunyada kwa Aedomu ndi kuwonongedwa kwao

1Izi ndi zimene Obadiya adaona m'masomphenya.

Naŵa mau a Ambuye Chauta onena za Aedomu.

Chauta adatuma wamthenga wake

kwa anthu a mitundu yonse,

ndipo tidamva mau ake, adati,

“Konzekani, tiyeni tikamenyane nkhondo ndi Aedomu.”

2Chauta akuuza Aedomu kuti,

“Ndithu ndidzakutsitsani kotheratu,

anthu a mitundu yonse adzakunyozani kwambiri.

3Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada.

Likulu lanu lili pakati pa matanthwe,

mumakhala pa mapiri aatali.

Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’

4Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga,

ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi,

ndidzakutsitsanibe pansi.”

Akutero Chauta.

5“Akuba akabwera usiku,

amangotengako zimene akufuna.

Okolola akamathyola zipatso,

amasiyako zina.

Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu.

6Onani m'mene alisakazira dziko la Esau,

ndi m'mene achifunkhira chuma chake chonse.

7Ogwirizana nanu akunyengani,

akupirikitsani m'dziko mwanu.

Okuthandizani pa nkhondo akugonjetsani.

Abwenzi anu apamtima akutcherani msampha,

mwathedwa nzeru tsopano.”

8Chauta akuti,

“Nthaŵi imeneyo ndidzaononga anzeru onse a ku Edomu,

ndidzathetsa kuchenjera konse kwa zidzukulu za Esau.

9Ngwazi za ku Temani zidzachita mantha,

ankhondo onse adzaphedwa ku mapiri a Esau.

Zolakwa za Aedomu

10“Aedomu inu, chifukwa cha zankhanza

zimene mudachita abale anu, zidzukulu za Yakobe,

adzakuchititsani manyazi ndi kukuwonongani mpaka muyaya.

11Munkangoonerera pamene adani ankaŵalanda chuma chao,

munkachita ngati kuvomerezana nawo,

amene ankaloŵa pa zipata za Yerusalemu,

namagaŵana chumacho.

12Inu simukadayenera kuŵanyodola abale anu Ayuda

chifukwa cha tsoka lao.

Simukadayenera kukondwerera kuwonongeka kwao.

Simukadayenera kuŵaseka

pamene iwo anali m'mavuto.

13Pa tsiku lao la tsoka

simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga.

Pa tsiku lao la tsoka

simukadayenera kuŵanyodola.

Pa tsiku lao la tsoka

simukadayenera kulanda chuma chao.

14 Yes. 34.5-17; 63.1-6; Yer. 49.7-22; Ezek. 25.12-14; 35.1-15; Amo. 1.11, 12; Mal. 1.2-5 Simukadayenera kudikira pa mphambano za miseu

kuti mugwire anthu othaŵa.

Pa tsiku lao la tsoka

simukadayenera kupereka anthu ao otsala kwa adani.

Tsiku la Chauta

15“Posachedwapa lifika tsiku la Chauta

pamene Iye adzaweruza mitundu yonse ya anthu.

Aedomu inu, adzakuchitani zomwe mudaŵachita ena.

Zimene mudachitazo zidzakubwererani.

16Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa

pa phiri langa loyera,

koma mitundu ina ya anthu

idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira.

Idzachita kugugudiza chikhocho

kenaka nkuzimirira pomwepo.

Israele adzapambana

17“Koma pa phiri la Ziyoni padzakhala ena opulumuka,

ndipo phirilo lidzakhala loyera.

Pamenepo fuko la Yakobe lidzalandira choloŵa chakechake.

18Fuko la Yakobe lidzakhala ngati moto,

fuko la Yosefe lidzakhala ngati malaŵi a moto,

fuko la Esau lidzakhala ngati ziputu.

Adzaŵatentha ndi kuŵapsereza,

ndipo sipadzapulumuka munthu aliyense.”

Akutero Chauta.

19Ayuda akumwera adzalandira phiri la Esau,

akuzambwe adzalandira dziko la Afilisti.

Akumpoto adzalandira dziko la Efuremu

ndi likulu lake Samariya,

ndipo Abenjamini adzalandira dziko lakuvuma la Giliyadi.

20Aisraele amene anali ku ukapolo

adzalandira dziko la Kanani

mpaka kumpoto ku Zarefati.

A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi

adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu.

21Ngwazi zochokera ku Yerusalemu

zidzagonjetsa ndi kumalamulira dziko la Edomu

ndipo ufumu wonse udzakhala wa Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help