14Mau a m'kalatayo ankayenera kudziŵika m'dera lililonse kuti ndi lamulo ndithu. Motero adayenera kuŵalengeza kwa anthu a mitundu yonse, kuti akonzekere pa tsiku limenelo.
15Anthu amtokoma aja adapita mofulumira, mfumu itaŵalamula, ndipo adapereka lamulo ku Susa, likulu la dziko. Tsono mfumu ndi Hamani adakhala pansi nkumamwa. Koma anthu a ku Susa adagwidwa ndi nthumanzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.