Lev. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Masiku a chikondwerero chachipembedzo

1Chauta adauza Mose kuti,

2“Uza Aisraele kuti, ‘Masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene mudzaŵalengeza kuti akhale masiku oyera amisonkhano, masiku achikondwerero amene Ine ndaŵasankha, ndi aŵa:

3Eks. 20.8-10; 23.12; 31.15; 34.21; 35.2; Deut. 5.12-14 pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lalikulu la Sabata, lopumula, tsiku la msonkhano wopatulika. Musamagwira ntchito iliyonse. Limenelo likhale tsiku la Sabata la Chauta kulikonse kumene mukakhale.’

Za Paska(Num. 28.16-25)

4“Masiku achikondwerero osankhidwa a Chauta, masiku oyera amisonkhano amene mudzaŵalengeza pa nthaŵi yake, ndi aŵa:

5Eks. 12.1-13; Deut. 16.1, 2 pa mwezi woyamba, tsiku la 14 la mweziwo, madzulo ake, ndi tsiku la Paska ya Chauta.

6Eks. 12.14-20; 23.15; 34.18; Deut. 16.3-8 Ndipo tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku la chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, lolemekezera Chauta. Pa masiku asanu ndi aŵiri muzidya buledi wosafufumitsa.

7Pa tsiku loyamba muchite msonkhano wopatulika, musagwire ntchito yotopetsa.

8Koma mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zotopetsa.”

9Chauta adauzanso Mose kuti,

10“Uza Aisraele kuti, ‘Mukakaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo ndi kukakolola za m'minda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa zoyambirira kucha mwa zokolola zanu.

11Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Chauta, kuti inuyo mulandiridwe. Auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata.

12Pa tsiku limene muweyule mtolowo, muperekenso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi wopanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta.

13Chopereka cha chakudya yopereka pamodzi ndi nkhosayo ikhale makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa yopereka pamodzi ndi nkhosayo, ikhale ya vinyo wokwanira ngati lita limodzi.

14Musadye buledi kapena tirigu wouma kapena wamuŵisi tsikuli lisanafike, mpaka mutabwera nayo nsembe kwa Mulungu wanu. Limeneli ndilo lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.’

Za chikondwerero chazokolola(Num. 28.26-31)

15 Eks. 23.16; 34.22; Deut. 16.9-12 “Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, pamene mudadzapereka mtolo wanu uja wa chopereka choweyula pamaso pa Chauta, muŵerenge milungu isanu ndi iŵiri yathunthu,

16ndiye kuti masiku asanu mpaka tsiku lotsatana ndi la Sabata lachisanu ndi chiŵiri. Patapita masiku amenewo, mupereke chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta.

17M'nyumba mwanu mutenge buledi muŵiri wa ufa wokwanira makilogaramu aŵiri, kuti amuweyule. Akhale wa ufa wosalala, ndipo aphikidwe ndi chofufumitsira, kuti akhale mphatso yoyamba yopereka kwa Chauta.

18Pamodzi ndi bulediyo, muperekenso anaankhosa asanu ndi aŵiri a chaka chimodzi opanda chilema, ndi likonyani lang'ombe lamphongo ndi nkhosa ziŵiri zamphongo. Zimenezi zikhale nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndiponso chopereka cha chakumwa. Zonsezo zikhale nsembe yopsereza ya fungo lokomera Chauta.

19Muperekenso tonde mmodzi ngati nsembe yopepesera machimo, ndi anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi ngati nsembe yachiyanjano.

20Wansembe aziweyule, pamodzi ndi buledi wa mphatso yoyamba uja, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta, pamodzi ndi anaankhosa amphongo aŵiri aja. Zimenezi ndi zopatulika zopereka kwa Chauta zokhalira ansembe.

21Tsono pa tsiku lomwelo mulengeze, ndipo muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kulikonse kumene mukakhale pa mibadwo yanu yonse.

22 Lev. 19.9, 10; Deut. 24.19-22 “Pamene mukolola dzinthu m'dziko mwanu, musakolole munda wanu mpaka m'malire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndiponso alendo. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”

Za chikondwerero cha chaka chatsopano(Num. 29.1-6)

23Chauta adauza Mose kuti,

24“Uza Aisraele kuti, ‘Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzilisunga kuti likhale tsiku lalikulu lopumula, tsiku lachikumbutso, lolengezedwa ndi malipenga, tsiku la msonkhano wopatulika.

25Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta.’ ”

Za tsiku lopepesera machimo(Num. 29.7-11)

26 Lev. 16.29-34 “Chauta adauza Mose kuti,

27‘Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lochita mwambo wopepesera machimo. Imeneyo ikhale nthaŵi yanu yochita msonkhano wopatulika. Musale zakudya, ndipo mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta.

28Musagwire ntchito pa tsiku limeneli, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wopepesera, wopepeseradi machimo anu pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.

29Aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake.

30Aliyense amene agwire ntchito pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga ameneyo pakati pa anthu a mtundu wake.

31Musagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.

32Likhale ngati tsiku lalikulu la Sabata lopumula kwa inu, ndipo musale zakudya. Pa tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, kuyambira madzulo ake mpaka madzulo ena otsatira, musunge tsikulo monga ngati la Sabata.’ ”

Za chikondwerero chamisasa

33 Deut. 16.13-15 Chauta adauza Mose kuti,

34“Uza Aisraele kuti, ‘Kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa masiku asanu ndi aŵiri, pazikhala chikondwerero chamisasa cholemekeza Chauta.

35Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa.

36Pa masiku asanu ndi aŵiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Chauta. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano wopatulika ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Umenewu ndi msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zotopetsa.’

37“Ameneŵa ndi masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene muziŵalengeza kuti ndi nthaŵi ya msonkhano wopatulika. Masiku ameneŵa muzipereka kwa Chauta nsembe zapamoto, monga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zanyama, ndi zopereka za chakumwa, iliyonse pa tsiku lake.

38Mupereke zimenezo pamodzi ndi nsembe za pa tsiku la Sabata la Chauta, mphatso zanu, nsembe zanu zonse zolumbirira ndi nsembe zanu zonse zaufulu, zimene mumapereka kwa Chauta.

39“Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mutakolola dzinthu m'dziko mwanu, muchite chikondwerero cha Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku loyamba likhale tsiku lalikulu lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu likhalenso tsiku lalikulu lopumula.

40Pa tsiku loyamba mutenge zipatso zabwino ndithu, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondodzi yakumtsinje, ndipo mukondwere pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, masiku asanu ndi aŵiri.

41Chaka chilichonse, masiku asanu ndi aŵiriwo musamale kuti akhale achikondwerero, olemekeza Chauta. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yonse. Muzilisunga pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri.

42Muzikhala m'misasa masiku asanu ndi aŵiri. Onse amene ali mbadwa m'dziko la Israele azikhala m'misasa,

43kuti mibadwo yanu idzadziŵe kuti ndine amene ndidakhalitsa Aisraele m'misasa, pamene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”

44Umu ndimo m'mene Mose adafotokozera kwa Aisraele za masiku achikondwerero osankhidwa, olemekeza Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help