1Ndine, Paulo, amene mwa kufuna kwa Mulungu ndidaitanidwa kuti ndikhale mtumwi wa Khristu Yesu. Ndili pamodzi ndi mbale wathu, Sostene.
2 wina akuti, “Ine ndine wa Kefa,” winanso akuti, “Ine ndine wa Khristu.”
13Kodi Khristu wagaŵika? Kodi adakuferani pa mtanda ndi Paulo? Kodi mudabatizidwa m'dzina la Paulo?
14 ndi Gayo basi.
15Motero palibe amene anganene kuti adabatizidwa m'dzina langa.
16 pamene Agriki amafunafuna nzeru.
23Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa.
24Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu.
25Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
26Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka.
27Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu.
28Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni.
29Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake.
30Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.
31Yer. 9.24 Nchifukwa chake, monga Malembo anenera, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.