Deut. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Musadzapereke ng'ombe kapena nkhosa yachilema ngati nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Musadzapereke nyama iliyonse yopunduka, chifukwa Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.

2Mwina padzapezeka kuti mu mzinda wina umene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani, muli munthu wina wamwamuna kapena wamkazi amene wachimwira Chauta, Mulungu wanu,

3Eks. 22.20 naphwanya chipangano chake, popembedza ndi kutumikira milungu ina, monga dzuŵa, mwezi kapena nyenyezi, zimene ndidaletsa kuti asazipembedze.

4Mukamva kuti chinthu chotere chachitika, mufufuze bwino nkhani imeneyo, ndipo mukapeza kuti choipa choterechi chachitikadi mu Israele,

5mumgwire mwamunayo kapena mkaziyo ndi kupita naye ku zipata za mzinda wanu ndipo mumphere kunja kwa mzinda pakumponya miyala.

6Num. 35.30; Deut. 19.15; Mt. 18.16; 2Ako. 13.1; 1Tim. 5.19; Ahe. 10.28 Munthuyo aphedwe pokhapokha patapezeka mboni ziŵiri kapena zitatu. Asaphedwe chifukwa cha umboni wa munthu mmodzi yekha.

71Ako. 5.13 Ziyambe ndi mbonizo kuponya miyala. Pambuyo pake anthu onse amponye miyala munthuyo. Motero chinthu choipacho mudzachichotsa pakati panu.

8Milandu yophana, yolimbirana zinthu, kapena yopwetekana m'mizinda mwanu, ikaŵavuta aweruzi anu, mupite ku malo achipembedzo aja osankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu,

9ndipo mupereke mlandu wanuwo kwa ansembe Achilevi ndi kwa muweruzi amene ali pa ntchito pa nthaŵi imeneyo. Ndipo iwowo agamule mlanduwo.

10Iwowo atagamula, inu muyenera kungochita zomwe akuuzani ku malo osankhidwa ndi Chauta.

11Muvomere chiweruzo chao, ndipo mutsate malangizo ao onse, osapotokera kumanja kapena kumanzere.

12Aliyense wosamvera wansembe amene akutumikira Chauta, Mulungu wanu, kapena wosamvera muweruzi, aphedwe. Mwa njira imeneyi mudzachotsa choipa pakati pa Aisraele.

13Tsono aliyense amene adzamve zimenezi adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kuchitanso zotere.

Za malangizo onena za mfumu

14 1Sam. 8.5 Mutaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo, ndipo mukadzafuna kuti mukhale ndi mfumu monga ili nayo mitundu ina yozungulira,

15mfumu imeneyo idzakhale munthu wosankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu. Adzakhale munthu wa mtundu wanu. Musadzasankhe mlendo kuti akhale mfumu yanu, ameneyo si mbale wanu.

161Maf. 10.28; 2Mbi. 1.16; 9.28 Mfumuyo isadzakhale ndi akavalo ambiri ndipo isadzatume anthu ku Ejipito kukagula akavalo, popeza kuti Chauta adakuuzani kuti, “Musadzabwererenso kumeneko.”

171Maf. 11.1-8; 1Maf. 10.14-22, 27; 2Mbi. 1.15; 9.27 Mfumu isadzakhale ndi akazi ambiri kuti mtima wake ungadzapotoke. Ndipo isadzadzikundikire siliva ndi golide wambiri.

18Munthuyo ataloŵa mu ufumu wakewo, adzalembe m'buku lakelake malamulo a Mulunguŵa ochokera mu buku la malamulo limene lili m'manja mwa ansembe Achilevi.

19Buku limeneli adzalisunge ndipo azidzaŵerengamo pa moyo wake wonse, kuti adzaphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wake, pakutsata mokhulupirika zonse zolembedwa m'bukumo.

20Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help