1Chauta ndi wamkulu,
ndi woyenera kumutamanda kwambiri.
Timuyamike mu mzinda wake,
pa phiri lake loyera,
2 Mt. 5.35 mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu,
wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi.
Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu,
ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.
3Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo,
pakuti Iye amakhala m'kati mwa malinga ake.
4Mafumu adasonkhana,
adafuna kuuthira nkhondo pamodzi.
5Atangopenya mzindawo adadzidzimuka, adachita mantha,
nathaŵa chinambalala.
6Adanjenjemera koopsa,
ndipo adamva ululu
wonga wa mkazi wovutika pa nthaŵi yochira.
7Inu Mulungu mudaŵaononga,
monga momwe mphepo yakuvuma ija
imapasulira zombo zopita ku Tarisisi.
8Zimene ife tidazimva,
taziwona zomwezo mu mzinda wa Chauta Wamphamvuzonse,
mzinda wa Mulungu wathu,
umene adaukhazikitsa mpaka muyaya.
9Tikakhala m'Nyumba mwanu, Inu Mulungu,
timalingalira za chikondi chanu chosasinthika.
10Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse,
monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi.
Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse.
11Anthu okhala mu Ziyoni akondwe.
A ku Yuda asangalale
chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama.
12Zungulirani Ziyoni yense,
inde zungulirani mzinda wonsewo,
ndipo muŵerenge nsanja zake.
13Yang'anani bwino machemba ake,
penyetsetsani malinga ake,
kuti mudzathe kusimbira mbadwo wakutsogolo.
14Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere,
ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.