1Patapita masiku aŵiri, Davide ndi anthu ake adafika ku Zikilagi. Tsono adapeza kuti Aamaleke anali atasakaza dera la kumwera kwa Yuda ndi kuthira nkhondo mzinda wa Zikilagi. Adagonjetsa mzindawo, nauthira moto.
2Adatenga akazi kuti akhale akapolo, pamodzi ndi onse amene anali m'menemo, aang'ono ndi aakulu omwe. Sadaphepo ndi mmodzi yemwe, koma adaŵatenga amoyo napita nawo.
3Davide ndi anthu ake atafika kumzindako adaupeza utapsa, ndipo akazi ao ndi ana anali atatengedwa ukapolo.
4Tsono Davide ndi anthu ake adalira mokweza, mpaka mphamvu zolirira zidaŵathera.
51Sam. 25.42, 43 Nawonso akazi a Davide anali atatengedwa ukapolo. Maina ao anali Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimele.
6Davide adavutika koopsa, pakuti anthu ankakamba zoti amponye miyala, chifukwa cha chisoni chao pokumbukira ana ao aamuna ndi aakazi. Koma Davide adapeza mphamvu mwa Chauta, Mulungu wake.
7 1Sam. 22.20-23 Pamenepo Davide adauza wansembe Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, kuti, “Undipatse efodi ija.” Abiyatara adampatsa.
8Tsono Davide adapempha nzeru kwa Chauta nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondo la Aamaleke? Kodi ndidzaŵapambana?” Chauta adamuyankha kuti, “Litsatire, pakuti udzalipambana ndithu ndipo udzaŵapulumutsa akapolowo.”
9Choncho Davide adanyamuka pamodzi ndi anthu 600 amene anali naye. Ndipo adakafika ku mtsinje wa Besori nasiyako anthu ena.
10Pamodzi ndi anthu 400 adapitirira kuŵalondola Aamalekewo, koma anthu 200 amene anali atatopa, adatsalira m'mbuyo, pakuti sadathe kuwoloka mtsinje wa Besori uja.
11Anthu amene anali ndi Davide, akuyenda m'njira, adapeza Mwejipito, nabwera naye kwa Davide. Tsono adampatsa buledi naadya. Adampatsanso madzi akumwa,
12chidutswa cha keke yankhuyu, ndi nchinchi ziŵiri za mphesa zoumika. Iyeyo atadya, moyo wake udatsitsimuka, pakuti sadaadya chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, masiku atatu athunthu.
13Davide adafunsa munthuyo kuti, “Kodi iwe ndiwe munthu wa yani? Ndipo ukuchokera kuti?” Munthuyo adati, “Ndine Mwejipito, kapolo wa Mwamaleke. Mbuyanga adandisiya masiku atatu apitaŵa poti ndinkadwala.
14Tinkathira nkhondo dera la kumwera kwa Yuda, ku maiko a Akereti, ndi dera la Akalebe. Mwakuti tidatentha mzinda wa Zikilagi.”
15Davide adamufunsa kuti, “Kodi ungandiperekeze ku gulu lankhondo limenelo?” Munthuyo adati, “Muyambe mwalumbira kwa Mulungu kuti simundipha kapena kundipereka kwa mbuyanga. Mukatero ndikuperekezani ku gulu lankhondo limenelo.”
16Choncho uja adaperekeza Davide kumeneko. Nthaŵi imeneyo Aamalekewo anali atamwazikana ponseponse. Analikudya, kumwa ndi kuvina, chifukwa cha zofunkha zimene adaatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Yuda.
17Tsono Davide ndi anthu ake adaŵathira nkhondo namenyana nawo kuyambira mbandakucha mpaka madzulo. Sadapulumukepo Mwamaleke ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu 400 amene adakwera pa ngamira, nathaŵa.
18Motero Davide adalanditsa zinthu zonse zimene adaatenga Aamaleke. Ndipo adapulumutsanso akazi ake aŵiri aja.
19Panalibe kanthu kalikonse kamene kadasoŵapo. Adalanditsa ana aamuna ndi ana aakazi, ndiponso chilichonse chimene chidaatengedwa.
20Adalanditsanso nkhosa zonse ndi ng'ombe zomwe. Ndipo anthu ankakusa zoŵetazo namati, “Izi ndi za Davide.”
21Pambuyo pake Davide adakafika kwa anthu 200 otopa kwambiri ndi osathanso kuyenda aja, amene adaaŵasiya ku mtsinje wa Besori. Iwo adanyamuka napita kukakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye aja. Davide adaŵayandikira naŵalonjera.
22Pamenepo anthu ena oipa mtima ndi opandapake a m'gulu la amene adaapita ndi Davide aja, adati, “Chifukwa chakuti sadapite nafe, sitiŵapatsako zofunkha zimene talanditsazi, kungopatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake, ndipo achoke.”
23Koma Davide adaŵauza kuti, “Musachite choncho, abale anga, ndi zinthu zimene Chauta watipatsa. Chautayo watisunga ndi kupereka m'manja mwathu gulu lankhondo limene lidabwera kudzamenyana nafe.
24Ndani angakuvomerezeni pa zimenezi? Munthu amene adapita ku nkhondo ndiponso munthu amene ankasunga katundu, onsewo ayenera kulandira zigawo zao mofanana.”
25Tsono Davide adagamula kuti njira imeneyi ikhale lamulo lokhazikika pakati pa Aisraele, kuyambira tsiku limenelo mpaka pano.
26Davide atafika ku Zikilagi, adapatulako zofunkha kusungira abwenzi ake, atsogoleri a ku Yuda, nauza aliyense kuti, “Nayi mphatso yanu yotapa pa zolanda kwa adani a Chauta.”
27Mphatsozo zidaperekedwa kwa anthu a ku Betele, a ku Ramoti kumwera kwa Yuda, a ku Yatiri,
28a ku Aroere, a ku Sifimoti, a ku Esitemowa,
29a ku Rakala, a ku mizinda ya fuko la Ayeramiyele, a ku mizinda ya fuko la Akeni,
30a ku Horoma, a ku Borasani, a ku Ataki
31a ku Hebroni ndiponso ku malo onse kumene Davide ankayenderako pamodzi ndi anthu ake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.