Esr. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hamani akonzekera kuchita Mordekai chiwembu

1Usiku umenewo mfumu sidathe kugona. Idalamula kuti buku lolembamo mbiri ya zinthu zimene zinkachitika kale libwere. Litabwera, wina adaliŵerenga pamaso pa mfumu.

2Tsono m'bukumo adapezamo mau akuti Mordekai adaulula za Bigitana ndi Teresi, aŵiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalonda pa khomo la mfumu, ndipo ankafuna kupha mfumu Ahasuwero.

3Apo mfumu idafunsa kuti, “Kodi Mordekai adamchitira ulemu ndi kumpatsa ukulu wotani pa zimenezi?” Atumiki a mfumu amene ankamutumikira adati, “Sadamchitirepo nkanthu komwe.”

4Mfumu idafunsa kuti, “Kodi ndani ali m'bwalomo?” Tsono pamenepo nkuti Hamani atangoloŵa m'bwalo la kunja kwa nyumba ya mfumu, kuti akauze mfumu zokapachika Mordekai pa mtengo umene adaamkonzera uja.

5Ndiye atumiki a mfumu adauza mfumuyo kuti, “Ndi Hamani amene waima m'bwalomo.” Mfumuyo idati, “Mloŵetseni.”

6Hamani ataloŵa, mfumu idamufunsa kuti, “Kodi nkumuchitira chiyani munthu amene mfumu yafuna kuti impatse ulemu?” Hamani adayamba kuganiza kuti, “Kodi ndaninso amene mfumu ingafune kumchitira ulemu koposa ine?”

7Tsono adauza mfumu kuti, “Munthu amene inu amfumu mwafuna kuti mumpatse ulemu, mumchitire izi: Tumani anthu,

8abwere ndi zovala zaufumu zimene amfumu amavala, ndi kavalo amene amfumu amakwerapo, amene ali ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake.

9Zovalazo ndi kavaloyo azipatse mmodzi mwa akalonga anu olemekezeka. Iyeyo amuveke munthuyo amene inu mwafuna kuti mumchitire ulemu. Kenaka amuyendetse m'miseu yamumzinda atamkweza pa kavaloyo, akufuula patsogolo pake kuti ‘Onanitu m'mene amamchitira munthu amene mfumu yafuna kuti impatse ulemu.’ ”

10Apo mfumu idamuuza Hamani kuti, “Fulumira, katenge zovalazo ndi kavalo monga momwe waneneramu. Umchitire zimenezo Mordekai, Myuda uja, amene akukhala pa chipata cha mfumu. Pasasoŵeke kanthu kalikonse pa zonse zimene watchulazi.”

11Choncho Hamani adatenga zovalazo ndi kavalo, ndipo adaveka Mordekai nayamba kumuyendetsa m'miseu yonse ya mumzindamo atamkweza pa kavalo, akulengeza kuti, “Onanitu m'mene amamchitira munthu amene mfumu yafuna kuti impatse ulemu.”

12Pambuyo pake Mordekai adabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani adapita msangamsanga kunyumba kwake akulira, atafundira kumutu.

13Kumeneko adakafotokozera mkazi wake Zeresi pamodzi ndi abwenzi ake onse, zonse zimene zidamgwera. Apo anthu ake anzeru pamodzi ndi mkazi wake Zeresi adamuuza kuti, “Mwayambapotu kugonja pamaso pa Mordekai. Tsono poti iye uja ndi Myuda, palibenso chimene mungachitepo kuti mumpambane. Kosapeneka konse mudzagwa ndithu pamaso pake basi.”

14Ameneŵa akulankhula zimenezi ndi Hamani, adindo ofulidwa a mfumu adafika, namtenga Hamani uja mofulumira, kupita naye ku phwando limene Estere adaakonza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help