1Ndani angafanefane ndi munthu wanzeru?
Ndani angadziŵe kutanthauza zinthu?
Munthu nzeru zake zimampatsa chimwemwe,
ndipo ukali umachoka pankhope pake.
Za kumvera mfumu2Uzimvera lamulo la mfumu, ndipo chifukwa cha lumbiro lako kwa Mulungu usade nkhaŵa.
3Zinthu zikapanda kuikondweretsa mfumu, uchoke pamaso pake mwamsanga, pakuti imachita chilichonse chimene chikuikomera.
4Pajatu mau a mfumu ndi opambana. Ndani angafunse kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”
5Womvera malamulo ake sadzaona vuto lililonse. Munthu wanzeru amadziŵa nthaŵi yake ndi njira yake yochitira zonse.
6Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi kachitidwe kake, ngakhale kuti mavuto ake a munthu amamupsinja kwambiri.
7Palibe amene amadziŵa zimene zilikudza. Palibe amene angafotokozere zakutsogolo.
8Monga munthu alibe mphamvu zolamulira mpweya wa moyo, chonchonso alibe mphamvu zolamulira tsiku la kufa kwake. Nkhondo sithaŵika, tsono anthu ochita zoipa, kuipa kwaoko sikudzaŵapulumutsa.
Kuweruzidwa kwa anthu oipa9Zonsezi ndidaziwona pamene ndinkalingalira mumtima mwanga zonse zimene zimachitika pansi pano. Nthaŵi zonse pali ena amene amalamulira anzao mwankhanza.
10Pambuyo pake ndidaona oipa akuikidwa m'manda. Iwowo kale ankaloŵa ndi kumatuluka m'malo oyera, ndipo mumzindamo anthu ankaŵatamanda m'mene ankachita zinthu zoterezi. Zimenezinso nzachabechabe.
11Oweruza akamachedwetsa chilango cha anthu opalamula, anthu ena amalimba mtima nkumafuna kuti ayambe kuchita zoipa nawonso.
12Ngakhale kuti wochimwa amati akachita zoipa kambirimbiri, amakhalabe moyo nthaŵi yaitali, komabe ndikudziŵa kuti omvera Mulungu ndiwo amene zinthu zidzaŵayendere bwino, poti ndi amene amamlemekeza.
13Koma oipawo zinthu sizidzaŵayendera bwino, ndipo moyo wao udzakhala wosakhalitsa ngati mthunzi, poti samvera Mulungu.
14Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika pansi pano. Chinthucho ndi ichi: mwina anthu abwino amalangidwa ngati ochita zoipa, pamene oipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. Ndikuti zimenezinso nzachabechabe.
15Nchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinthu chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake, amene Mulungu wampatsa pansi pano.
Njira za Mulungu nzosafufuzika16Ndinkaikapo mtima kuti ndidziŵe nzeru ndi kumvetsa ntchito zimene zikuchitika pansi pano, osapeza tulo usana ndi usiku.
17Ndipo ndidaona ntchito zonse za Mulungu. Palibe munthu amene angathe kuzitulukira zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse chotani kuzimvetsa, sadzafikapo. Ngakhale munthu wanzeru anene kuti akudziŵa zinthu, nkosatheka kuti azitulukire.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.