Esr. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ukulu wa Ahasuwero ndi Mordekai

1Mfumu Ahasuwero ankakhometsa msonkho m'dziko mwake ndiponso ku zilumba za m'nyanja.

2Ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake ndiponso ukulu wake, pamodzi ndi zonse zofotokoza za kukwezedwa kwa Mordekai ndi za ulemu wake, zimene mfumu adamkweza nazo, zonsezi zidalembedwa m'buku la Mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi a ku Persiya.

3Zoonadi, Mordekai, Myuda uja, anali wachiŵiri kwa mfumu Ahasuwero. Anali wamkulu ndiponso womveka pakati pa Ayuda, wokondedwa ndi unyinji wa abale ake, pakuti ankaŵachitira zabwino anthu a mtundu wake ndi kuŵafunira zamtendere.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help