1Pambuyo pake mafuko onse a Aisraele adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi.
2Kale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo nkubwera nawonso. Ndipo Chauta adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya Israele.’ ”
3Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono mfumu Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse.
4
21Afilisti adasiya mafano ao kumeneko, ndipo Davide ndi anthu ake adatenga mafanowo napita nawo kwao.
22Nthaŵi ina Afilisti adabweranso, nandanda m'chigwa chija cha Refaimu.
23Davide atafunsa Chauta, adamuyankha kuti, “Usakaŵathire nkhondo kumaso. Uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija.
24Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo ukakonzeke, chifukwa ndiye kuti Chauta wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.”
25Davide adachitadi monga momwe Chauta adaamlamulira, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kuyambira ku Geba mpaka ku Gezere.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.