Mphu. 42 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Koma zimene ndinene tsopanozi usachite

nazo manyazi,

ndipo usachimwe chifukwa choopa anthu ena.

2Usachite manyazi ndi Malamulo ndiponso

chipangano cha Mulungu Wopambanazonse,

Usachite manyazi kuweruza molungama

ngati mlandu wakomera munthu wosapembedza.

3Usachite manyazi kuŵerengerana bwino ndalama

ndi bwenzi lako kapena mnzako woyenda naye,

kapena kugaŵana nawo chuma chosiya ena.

4Usachite manyazi kugwiritsa bwino ntchito

miyeso yopimira zinthu ndi kupezapo phindu

lalikulu pena laling'ono.

5Usachite manyazi kupeza phindu pa malonda

kapena kulanga moyenera ana ako,

kapena kukwapula kwamphamvu kapolo woipa.

6Ngati mkazi ngwosakhulupirika,

kapena antchito ngochuluka,

ndi bwino kumakhoma mosunga zinthu zako.

7Zonse zimene umaikiza,

uziŵerengere bwino ndi kuziyesa,

ndipo ulemberetu zonse

zimene walandira kapena kupereka.

8Usachite manyazi kulangiza munthu wosadziŵa

kapena wopusa,

kapena kuthandiza nkhalamba yaimvi ikayambana

ndi anyamata.

Ukatero udzadziŵika kuti ndiwedi munthu wodziŵa mwambo,

ndipo anthu onse adzakuvomereza.

Bambo azisamalira mwana wake wamkazi

9 Mphu. 7.24, 25; 26.10-12 Bambo nthaŵi zonse amakhala ndi nkhaŵa pa mwana

wake wamkazi.

Sagona tulo chifukwa choganiza za mwana wakeyo.

Amada nkhaŵa kuti mwana wake angakhalitse osakwatiwa,

ndipo amaopa kuti akadzakwatiwa,

mwina mwamuna wake adzaleka kumkonda.

10Mtsikana ali namwali, bambo wake amada naye nkhaŵa

kuti mwina munthu wina nkumuipitsa,

natenga pakati akali m'nyumba mwa bambo wakeyo.

Mwanayo akakwatiwa, bambo wake amaopa

kuti mwina sadzakhala wokhulupirika kwa mwamuna wake,

amadanso nkhaŵa kuti ngakhale akwatiwe,

mwina adzakhala chumba.

11Ngati mwana wako wamkazi ngwopulupudza,

umulonde bwino kuti adani ako angadzakuseke

ndipo anthu am'mudzimo angamakambe za iwe,

ndiponso kuti iye angakuchititse manyazi pamaso pa onse.

Za akazi

12Usamayang'anitsitse kukongola kwa mkazi aliyense,

ndipo usamati pakati pa anthu aakazi mbwerekete!

13Monga m'mene njenjete zimatulukira m'zovala,

ndi m'menenso kuipa kwa akazi kumatulukira mwa akaziwo.

14Kuipa kwa munthu wamwamuna kuli ndiponiko

kuposa kukoma mtima kwa munthu wamkazi,

chifukwa mkazi ndiye amachititsa manyazi ndi

kudzetsa manyozo.

II ZA ULEMERERO WA MULUNGUA: M'ZOLENGEDWA

15Tsopano ndikuti ndikukumbutseni ntchito za Ambuye,

ndi kufotokoza zinthu zimene ndidaona.

Mau a Ambuye ndiwo amapangitsa ntchito zao,

ndipo zolengedwa zonse zimatsata kufuna kwao.

16Monga dzuŵa limaŵalira zolengedwa zonse,

ulemerero wa Ambuye umadzaza zolengedwa zonse.

17Ngakhale Angelo omwe Ambuye sadaŵapatse mphamvu

zofotokozera ntchito zao zonse zodabwitsa,

zimene Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse adazichita,

kuti dziko lapansi likhale mu ulemerero wao.

18Ambuye amadziŵa zobisika m'nyanja yaikulu ndi

za m'mitima mwa anthu,

ndipo amaona zolinga zao zonse.

Paja Mulungu Wopambanazonse amadziŵa zonse,

ndipo amapenya zizindikiro za nyengo zonse.

19Amafotokoza zakale ndi zakutsogolo,

ndipo amaulula zinthu zobisika.

20Amadziŵa maganizo athu onse,

zolankhula zathu zonse nzosabisika kwa Iye.

21Adalongosola bwino ntchito zazikulu zonse za nzeru zake,

Iye amene alipo chikhalire ndi mpaka muyaya.

Sitingathe kumuwonjezerapo kapena kumchotserapo kanthu,

ndipo sasoŵa wina woti azimlangiza.

22Ntchito zake zonse nzosiririka kwambiri,

nzokongola kwabasi m'masomu.

23Zonsezi zilipo ndipo zidzakhalapo mpaka muyaya,

zonse zimamvera Iye pa cholinga chake.

24Zinthu zonse zimayenda ziŵiriziŵiri,

china choyang'anana ndi chinzake.

Palibe chinthu chimene adachipanga mosakwanira.

25Zonse zimatsimikiza zokoma za zinzake.

Ndani angatope nkuyang'ana ulemerero wake?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help