Eza. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adani ofuna kuletsa kumanga Nyumba ya Mulungu

1Adani a Yuda ndi a Benjamini adaamva kuti anthu obwerako ku ukapolo aja akumangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Aisraele.

22Maf. 17.24-41 Ndiye adadza kwa Zerubabele ndi kwa atsogoleri a mabanja, naŵauza kuti, “Mutilole kuti timange nawo, pakuti ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthaŵi ya Ezaradoni, mfumu ya ku Asiriya, amene adatifikitsa kuno.”

3Koma Zerubabele, Yesuwa, ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a m'dziko la Israele adaŵayankha kuti, “Sitikusoŵa chithandizo chanu pa ntchito iyi yomangira Nyumba Mulungu wathu. Koma ife tokha tidzammangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi, mfumu ya ku Persiya, adatilamula.”

4Atamva zimenezi anthu a m'dzikomo adayamba kutayitsa mtima Ayuda, ndi kuŵachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo.

5Adalemba akuluakulu ena kuti alepheretse cholinga chao cha pa ntchitoyo pa nthaŵi yonse ya Kirusi, mfumu ya ku Persiya, ngakhalenso mpaka pamene Dariusi, mfumu ya ku Persiya ankalamulira dzikolo.

Aletsa Ayuda kuti asapitirize kumanganso Yerusalemu

6 Esr. 1.1 Pamene mfumu Ahasuwero adayamba kulamulira dziko, adani aja adalemba kalata yoneneza nzika zija za ku Yuda ndi za ku Yerusalemu.

7Chimodzimodzinso pa nthaŵi ya Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Persiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabiyele ndi anzao ena, adalemba inanso kalata kwa Arita-kisereksesiyo. Kalatayo adailemba m'Chiaramu, ndipo poiŵerenga ankachita kutanthauzira.

8Kenaka Rehumu Bwanamkubwa ndi Simisai mlembi wake, nawonso adalemba yao kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi yoneneza anthu a ku Yerusalemu. Adalemba motere:

9“Kalatayi ikuchokera kwa Rehumu bwanamkubwa, mlembi Simisai ndi anzao aŵa: aweruzi, nduna ndi akuluakulu ena, anthu a ku Persiya ndi ku Ereki, ku Babiloniya, ndi ku Susa, m'dziko la Elami.

10Enanso ndi mitundu ina imene Osinapara, wamkulu ndi womveka uja, adaisamutsa ndi kuikhazika m'mizinda ya Samariya ndi kwinanso m'madera a m'chigawo chimene chili Patsidya pa Yufurate.”

11Mau ake a m'kalata imene adatumizayo ndi aŵa: “Zikomo, amfumu Arita-kisereksesi, ife atumiki anu, a m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, poyamba tikukupatsani moni.

12Amfumu, tikuti mudziŵeko kuti Ayuda omwe adabwera kuno kuchokera kwanuko, apita ku Yerusalemu. Akumanganso mzinda wopanduka ndi woipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonza maziko.

13Tsonotu amfumu, mudziŵe kuti akaumanganso mzinda umenewu ndi kumaliza kumanga makoma ake, ndiye kuti anthu aja adzaleka kukhoma msonkho ndi kupereka kasitomo kapena msonkho wa kanthu kena kalikonse, ndipo chuma choloŵa m'thumba la mfumu chidzachepa.

14Tsono popeza kuti ife ndife akadyere kwa mfumu, si bwino kuti tizingopenya zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nchifukwa chake tikutumiza mau kwa inu mfumu kuti mudziŵe zonse.

15Ndi bwino kuti pachitike kafukufuku m'buku la mbiri yakale ya makolo anu. M'buku lazakalemo mudzapeza ndi kuŵerengamo kuti mzinda umenewo ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zam'madera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuchita zoukira ulamuliro uliwonse. Nchifukwa chake mzinda umene uja adausandutsa bwinja.

16Tikukudziŵitsani inu amfumu kuti ngati mzinda umenewu aumanganso ndi kutsirizanso makoma ake, ndiye kuti inuyo simudzatha kumalamulirabe m'chigawo cha Patsidya pa Yufuratecho.”

Mfumu iyankha kalata

17Tsono mfumuyo idayankha kalatayo motere, “Bwanamkubwa Rehumu ndi mlembi Simisai, ndi anzanu ena amene akukhala ku Samariya ndi m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, ndikuti moni.

18Kalata imene mudatumiza, aiŵerenga pamaso panga momveka bwino.

19Ine nditalamula kuti afufuzefufuze nkhaniyi, kwapezekadi kuti mzinda umenewo udaaukira mafumu kale, ndipo kuti zaupandu ndi zoukira zinkachitikadi m'menemo.

20Mafumu amphamvu adakhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonsecho cha Patsidya pa Yufurate, namalandira kasitomo ndi msonkho pa kanthu kena kalikonse.

21Tsono inu mulembe lamulo loŵaletsa anthu amenewo kuti asamangenso mzinda umenewo, mpaka ine nditaloleza.

22Ndithu zimenezi musachedwetse. Nanga ndingalole bwanji kuti zoononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?”

23Kalata ya mfumu Arita-kisereksesiyo ataiŵerenga pamaso pa Rehumu ndi mlembi Simisai ndi anzao, iwowo adapita msangamsanga ku Yerusalemu, nakaŵaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirize ntchito yao.

24Hag. 1.1; Zek. 1.1Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu idalekeka mpaka chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, mfumu ya ku Persiya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help