1Chauta adauza Mose kuti,
2“Ulankhule ndi Aisraele kuti akupatse ndodo, fuko lililonse ndodo imodzi. Atsogoleri ao onse akupatse ndodo khumi ndi ziŵiri molingana ndi mafuko a makolo ao. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake,
3ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi. Pakuti payenera kukhala ndodo imodzi pa mtsogoleri aliyense wa fuko la makolo ake.
4Tsono ndodozo uziike m'chihema chamsonkhano patsogolo pa bokosi laumboni pamene ndimakumana nawe.
5Ndipo ndodo ya munthu amene nditi ndimsankhe idzaphuka. Motero sindidzalola kumvanso maŵiringulo amene Aisraele amachita otsutsana nawe.”
6Choncho Mose adalankhula ndi Aisraele. Ndipo atsogoleri onse adampatsa ndodozo, mtsogoleri aliyense ndodo imodzi molingana ndi mafuko a makolo ao, ndiye kuti ndodo khumi ndi ziŵiri pamodzi. Ndodo ya Aroni inali pakati pa ndodo zao.
7Mose adakaziika ndodozo pamaso pa Chauta m'chihema chaumboni.
8 Ahe. 9.4 M'maŵa mwake Mose adakaloŵa m'chihema chaumboni. Adangoona ndodo ya Aroni, ya fuko la Levi, itaphuka masamba nkuchitanso maluŵa, ndipo itabala zipatso zakupsa za mtundu wa matowo.
9Tsono Mose adatulutsa ndodo zonse zija pamaso pa Chauta ndi kuŵaonetsa Aisraele. Ataona, mtsogoleri aliyense adatenga ndodo yake.
10Apo Chauta adauza Mose kuti, “Kabwezere ndodo ya Aroni patsogolo pa bokosi laumboni. Uisunge kuti ikhale chenjezo kwa anthu oukira aja, kuti aleke kuŵiringulako, kuti angafe.”
11Mose adachita momwemo. Adatsatadi zomwe Chauta adalamula.
12Tsono Aisraele adauza Mose kuti, “Tatayika, tonsefe taferatu.
13Ngati munthu aliyense amene akuyandikira chihema cha Chauta alikufa, ndiye kuti tonsefe ndife akufa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.