Miy. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Zolinga zamumtima ndi za munthu,

koma zolankhula zake ndi zochokera kwa Chauta.

2Ntchito zake za munthu zimakhala zolungama

pamaso pake,

koma Chauta amaweruza zamumtima.

3Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta,

ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

4Chauta adapanga chinthu chilichonse

kuti chikhale ndi cholinga chake,

ngakhale anthu oipa, kuti aone tsiku la mavuto.

5Munthu aliyense wodzikuza amanyansa Chauta,

ndithu ameneyo sadzalephera kulangidwa.

6 Tob. 12.9 Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika,

munthu amakhululukidwa machimo ake.

Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa.

7Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta,

ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.

8 Tob. 12.8 Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono

uli ndi chilungamo

kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri

ulibe chilungamo.

9Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite,

koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe

a munthuyo.

10M'kamwa mwa mfumu mumatuluka chigamulo

chochokera kwa Mulungu.

Pakamwa pa mfumu sipalakwa pogamula mlandu.

11Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo

zikhale zachilungamo.

Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta.

12Kuchita zoipa kumanyansa mafumu,

pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wao.

13Mau oona amakondweretsa mfumu,

ndipo imamkonda munthu wolankhula chilungamo.

14Mfumu ikakwiya, ndiye kuti imfa ili pafupi,

koma munthu wanzeru amaupepesa mkwiyowo.

15Kukoma mtima kwa mfumu kumadzetsa moyo,

kuli ngati mitambo ya mvula yam'chilimwe.

16Kupata nzeru kumapambana kupata golide.

Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana

kukhala ndi siliva.

17Mseu wa munthu wolungama umapewa zoipa.

Munthu wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.

18Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko,

ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa.

19Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa

pakati pa anthu osauka,

kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.

20Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera

bwino,

ndi wodala amene amadalira Chauta.

21Wa mtima wanzeru amamutcha wozindikira bwino zinthu,

kulankhula kwake kokometsera

kumakulitsa mphamvu ya mau ake.

22Nzeru ndi kasupe wopatsa moyo kwa amene ali nazo,

koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa anthu opusa.

23Mtima wa munthu wanzeru umamlankhulitsa mau ochenjera,

nzeruzo zimakulitsa mphamvu ya mau ake.

24Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi,

amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

25 Miy. 14.12 Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu,

koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa.

26Njala ya munthu wantchito imamthandiza kulimbikira,

ndi njalayo imene imamkakamiza kuchita kanthu.

27Munthu wopandapake amakonzekera kuchita zoipa,

mau ake ali ngati moto wopsereza.

28 Mphu. 28.13-26 Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano,

kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.

29Munthu wandeu amakopa mnzake,

ndipo amamuyendetsa m'njira yoipa.

30Amene amatsinzinira masoŵa,

amalingalira zinthu zokhota,

amene amachita msunamo amadzetsa zoipa.

31Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero,

munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali.

32Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo,

amene amadzigwira mtima amapambana

msilikali wogonjetsa mzinda.

33Maere amaŵaponya m'funkha,

koma amene amaulula ndi Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help