Miy. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo,

koma mau ozaza amakolezera ukali.

2Mau a anthu anzeru amapatsa nzeru,

koma pakamwa pa opusa pamatulutsa zauchitsiru.

3Maso a Chauta ali ponseponse,

amayang'ana oipa ndi abwino omwe.

4Mau ofatsa amakhala ngati mtengo wopatsa moyo,

koma mau oipa amapweteka mtima.

5Chitsiru chimanyoza malangizo a bambo wake,

koma wochenjera amamvera chidzudzulo.

6Munthu wochita chilungamo amakhala ndi chuma chambiri,

koma zimene woipa amapindula zimamgwetsa m'mavuto.

7Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru,

koma mitima ya zitsiru siitero.

8Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta,

koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.

9Zochita za anthu oipa zimamnyansa Chauta,

koma wochita zachilungamo Chauta amamkonda.

10Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa.

Amene amadana ndi kudzudzula adzafa.

11Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika kwa Mulungu,

nanji tsono mitima ya anthu!

12Wonyada sakonda kumdzudzula,

sapitako kwa anthu anzeru.

13Mtima wosangalala umaonetsa nkhope yachimwemwe,

koma mtima wachisoni umaphwanya moyo.

14Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu

kudziŵa zambiri,

koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!

15Munthu wozunzika masiku ake onse amakhala oipa,

koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo

nthaŵi zonse.

16Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono

nkumaopa Chauta,

kupambana kukhala ndi chuma chambiri

nkupeza nacho mavuto.

17Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi,

kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa

pali chidani.

18Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano,

koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.

19Njira ya munthu waulesi ndi yoŵirira ndi minga,

koma njira ya munthu wolungama

imakhala ngati mseu wosalala.

20Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake,

koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

21Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru,

koma munthu womvetsa zinthu amatsata zolungama.

22Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika,

koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

23Kuyankha mokhoza kumakondwetsa munthu,

ndipo mau onena pa nthaŵi yake amakoma.

24Njira yopita ku moyo imakamufikitsa

ku ntchito zangwiro,

kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko.

25Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada,

koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye.

26Maganizo a anthu oipa amamnyansa Chauta,

koma mau a anthu olungama amamkondweretsa.

27Munthu wofunafuna phindu monyenga

amavutitsa banja lake,

koma munthu wodana ndi ziphuphu adzapeza bwino.

28Munthu wabwino amaganizira za m'mene ayankhire,

koma pakamwa pa munthu woipa pamatuluka

mau oipa okhaokha.

29Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima,

koma amamva pemphero la anthu achilungamo.

30Maso okondwa amasangalatsa mtima,

ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.

31Amene makutu ake amalandira bwino kudzudzula koyenera,

adzakhala m'gulu la anthu anzeru.

32Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha,

koma wovomera kudzudzula

amapindula nzeru yomvetsa zinthu.

33Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru,

ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu,

chili patsogolo nkudzichepetsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help