Yes. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizo

1Tsoka kwa iwe woonongawe,

iwe amene sadakuwononge.

Tsoka iwe wonyengawe,

amene wina aliyense sadakunyenge.

Iwe ukadzaleka kuwononga, adzakuwononga,

ukadzaleka kunyenga, adzakunyenga.

2Mutichitire chifundo, Inu Chauta,

tikukhulupirira Inu.

Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu

tsiku ndi tsiku,

ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto.

3Mukatulutsa liwu lanu longa bingu,

mitundu ya anthu imathaŵa.

Inu mukadzambatuka,

mitundu ya anthu imabalalika.

4Amakundika zokunkha monga m'mene zimachitira ziwala.

Anthu amalumphira zofunkhazo

monga m'mene limachitira dzombe.

5Chauta ndi wolemekezeka kwambiri,

pakuti akukhala pamwamba pa zonse.

Adzadzaza mzinda wa Ziyoni ndi chilungamo ndi ungwiro.

6Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu.

Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu,

luntha lambiri ndi nzerunso zambiri.

Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.

7Anthu ao olimba mtima akufuula m'miseu,

akazembe odzayesa kudzetsa mtendere akulira kwamphamvu.

8M'miseu yaikuluikulu muli zii, palibe odzeramo.

Zipangano zaphwanyidwa, mboni zanyozedwa,

ndipo palibenso kulemekezana.

9Dziko likulira ndipo likunka lilikutha.

Nkhalango za ku Lebanoni zafota,

ndipo chigwa chachonde cha Saroni

chasanduka chipululu.

Mitengo ya ku dera la Basani

ndi ya ku phiri la Karimele ikuyoyoka masamba.

Chauta achenjeza adani ake

10Chauta akunena kuti,

“Tsopano ndichitapo kanthu,

ndiwonetsa mphamvu zanga,

ndipo ndidzakhala wolemekezeka kwambiri.

11Inu mumaganiza zachabechabe,

ndipo zonse zimene mumachita nzopandapake.

Zotuluka m'kamwa mwanu zili ngati moto

umene udzakuwonongani inu nomwe.

12Anthu a mitundu ina adzakhala ngati miyala

yotenthedwa popanga njereza,

adzakhala ngati minga yodula, yotenthedwa pamoto.

13“Inu amene muli kutali,

imvani zimene ndachita.

Inu amene muli pafupi,

dziŵani mphamvu zanga.”

14Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha,

anthu osasamala za Mulungu akunjenjemera.

Akunena kuti,

“Ndani mwa ife angathe kupirira m'moto woonongawo?

Ndani mwa ife angathe kukhalamo m'moto wosatha?”

15Angathe kutero ndi amene amachita zolungama

ndi kulankhula zoona,

amene amakana phindu lolipeza monyenga,

amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu,

amene amatseka makutu kuti angamve mau

opangana za kupha anzao,

amene amatsinzina kuti angaone zoipa.

16Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa.

Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe.

Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.

Ulemerero wa zam'tsogolo

17Nthaŵi imeneyo mudzayang'ana mfumu yooneka mokongola,

ndipo mudzaona dziko labwino lotambasukira kutali.

18Mumtima mwanu muzidzalingalira

zimene zinkakuwopsani kale.

Muzidzati, “Ali kuti wokhometsa msonkho uja?”

19Simudzaonanso anthu amwano aja

amene chilankhulo chao nchosadziŵika,

chachilendo ndi chosamveka.

20Onani Ziyoni, mzinda wa zokondwerera

zathu zachipembedzo.

Maso anu adzaona Yerusalemu,

mzinda wamtendere, hema losasunthika.

Zikhomo zake sizidzazuka,

ndipo zingwe zake sizidzaduka.

21Kumeneko Chauta adzatiwonetsa ulemerero wake.

Adzakhala malo a mitsinje yaikulu ndi yaing'ono.

Ngalaŵa zankhafi sizidzapitapo,

ndipo zombo zazikulu sizidzayendapo.

22Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu.

Chauta ndiye wotilamula,

Chauta ndiye mfumu yathu,

ndiye amene adzatipulumutsa.

23Zingwe za zombo za adani athu zamasuka,

sizingathe kulimbitsa mlongoti wake,

ndipo matanga ake sangathe kufunyuluka.

Tsono zofunkha zathu zidzakhala zochuluka kwambiri,

kotero kuti pogaŵana, ndi opunduka omwe adzalandirako.

24Palibe ndi mmodzi yemwe m'dzikomo wodzanena kuti,

“Ndikudwala,” ndipo anthu onse akumeneko

machimo ao adzakhululukidwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help