Gen. 40 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yosefe amasula maloto a akaidi

1Patapita kanthaŵi, munthu woperekera vinyo pamodzi ndi wopanga buledi ku nyumba ya mfumu ya ku Ejipito, adalakwira mbuyao mfumu.

2Farao adaŵakwiyira kwambiri antchito ake aŵiriwo.

3Motero adaŵatsekera m'ndende, nakaŵaika m'manja mwa mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa mfumu uja, m'ndende momwe Yosefe ankasungidwa.

4Mkulu wa alonda uja adasankhula Yosefe kuti asamalire anthu aŵiriwo ndi kuŵalonda. Adakhalamo nthaŵi yaitali ndithu m'ndendemo.

5Usiku wina m'ndendemo, anthu aŵiri onse aja, woperekera vinyo uja ndi wophika buledi, adalota maloto. Aliyense mwa aŵiriwo adalota maloto ake a tanthauzo lakelake.

6Yosefe atabwera m'maŵa, adaona kuti nkhope zao zasinthika.

7Adaŵafunsa kuti, “Mwatani mukuwoneka ngati achisoni lero?”

8Onsewo adayankha kuti, “Aŵirife tonse talota maloto usiku wapitawu, ndipo pano palibe ndi mmodzi yemwe wotha kutimasulira malotowo.” Apo Yosefe adaŵauza kuti, “Ndi Mulungu yekhatu amene amapatsa nzeru zomasulira maloto. Tandiwuzani maloto anuwo.”

9Motero uja woperekera vinyoyu adayambapo kunena maloto ake, adati, “Ine ndinalota ndikuwona mtengo wamphesa,

10unali ndi nthambi zitatu. Masamba ake atangophukira, pomwepo panaoneka maluŵa, pambuyo pake panaonekanso mphesa zakupsa.

11Chikho cha Farao chinali m'manja mwanga; ine ndinatenga mphesazo nkufinyira m'chikhomo, ndipo ndinachipereka kwa Farao.”

12Yosefe adamuyankha kuti, “Tanthauzo lake la maloto ameneŵa nali: nthambi zitatuzo ndi masiku atatu.

13Pakangopita masiku atatu, Farao akutulutsa muno, akukhululukira, ndipo akubwezera pa ntchito yako. Tsono uzidzaperekera chikho kwa Farao monga momwe unkachitira kale.

14Komatu udzandikumbuke, zinthu zikadzakuyendera bwino. Chonde udzandikomere mtima ndi kutchula dzina langa kwa Farao, kuti ndidzatulule m'ndende muno.

15Inetu adachita chondiba, ndipo adabwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri. Tsono ngakhale kunoko, sindidachite kanthu kalikonse koti anditsekere nako m'ndende.”

16Wophika buledi uja nayenso adaona kuti tanthauzo la malotowo linali labwino, adauza Yosefe kuti, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi pamutu pangapa.

17M'nsengwa yapamwamba munali mitundu yambiri ya chakudya cha Farao, koma mbalame zinalikudya chakudyacho.”

18Yosefe adamuyankha kuti, “Kamasulidwe kake ka maloto ameneŵa ndi aka: nsengwa zitatu ndi masiku atatu.

19Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa muno, ndipo adzadula mutu wako. Tsono mtembo wako adzaupachika pa mtengo, ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.”

20Patangopitadi masiku atatu, padachitika phwando lokondwerera tsiku lobadwa Farao, ndipo Faraoyo adaitana nduna zake zonse. Tsono adamtulutsa uja woperekera vinyoyu pamodzi ndi wophika buledi yemwe uja. Aŵiri onse aja adaŵaimika pamaso pa nduna zake zija.

21Farao adamubwezera pa tchito yake woperekera vinyo uja.

22Koma wophika buledi uja adampachika, monga momwe Yosefe adaanenera pomasulira maloto ao aja.

23Komabe woperekera vinyo uja sadamkumbuke Yosefe, adangomuiŵaliratu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help