Deut. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Lamulo lalikulu

1Tsono aŵa ndi malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata, zimene Chauta, Mulungu wanu, adandilamula kuti ndikuphunzitseni. Muzikatsata zonsezi m'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo,

2nthaŵi zonse pamene muli moyo, inu ndi zidzukulu zanu. Muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniŵa, kuti pakutero mukakhale moyo nthaŵi yaitali.

3Inu Aisraele, mutchere khutu, ndipo muchenjere, mumveredi malamuloŵa. Tsono zinthu zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala mtundu wochuluka zedi ndi kumakhala m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezerani.

4 Mk. 12.29 Mverani, inu Aisraele, Chauta Mulungu wathu ndi mmodzi yekha.

5Mt. 22.37; Mk. 12.30; Lk. 10.27 Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.

6Deut. 11.18-20 Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.

7Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

8Amangeni pamikono panu, ndiponso muŵaike pa mphumi pakati pa maso anu.

9Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

Chenjezo kwa osamvera

10 Gen. 12.7; Gen. 26.3; Gen. 28.13 Chauta, Mulungu wathu, adalonjeza makolo anu aja Abrahamu, Isaki ndi Yakobe kuti adzakupatsani inu dziko limene lili ndi mizinda ikuluikulu ndi yachuma, imene inu simudaimange.

11Nyumba zake zidzakhala zodzaza ndi zinthu zabwino zimene inuyo simudaikemo. Zitsime zidzakhala zokumbiratu ndipo padzakhala minda yamphesa ndi yaolivi imene simudalime ndinu. Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limeneli, ndipo mukadzakhala ndi chakudya chambiri,

12musadzaiŵale Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, dziko laukapolo.

13Mt. 4.10; Lk. 4.8 Muziwopa Chauta, Mulungu wanu. Muzipembedza Iye yekha, ndipo mukamalumbira, muzitchula dzina lake lokha.

14Musamapembedza milungu ina, milungu imene amaipembedza anthu okhala mozunguliramu,

15popeza kuti mukatero, mkwiyo wa Chauta udzakuyakirani ngati moto, ndipo udzakuwonongani kwathunthu, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amene amakhala pakati panu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye.

16 Mt. 4.7; Lk. 4.12; Eks. 17.1-7 Musamupute Chauta, Mulungu wanu, monga mudachitira ku Masa kuja.

17Musamale kuti musunge malamulo onse amene Iye akupatsani.

18Muzichita zokhazo zimene Chauta akuti ndi zolungama ndi zabwino, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Mudzalandira dziko labwinolo limene Chauta adalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo anu.

19Adani anu mudzaŵapirikitsa, monga Chauta adalonjezera.

20Nthaŵi zakutsogoloko, ana anu adzakufunsani kuti, “Kodi chifukwa chiyani Chauta, Mulungu wathu, adakulamulani kuti muzimvera malamulo ndi malangizo ndi zina zonse zoyenera kuzitsatazi?”

21Tsono inu mudzaŵauze kuti, “Ife tidaali akapolo a mfumu ya dziko la Ejipito, koma Mulungu adatipulumutsa ndi mphamvu zake zazikulu.

22Ife tidapenya ndi maso athu Chauta akuchita zodabwitsa ndi zoopsa kuti alange Aejipito, mfumu yao ndi banja lao lonse.

23Mulunguyo adatitulutsa ife ku Ejipito, natifikitsa kuno ndi kutipatsa dziko lino, monga momwe adalonjezera kwa makolo athu.

24Pamenepo Mulungu wathu adatilamula kuti tizimvera malamulo onseŵa, ndiponso kuti tizimuwopa. Tikamatero, Iyeyo adzasunga mtundu wathu, ndipo adzautukula monga momwe akuchitiramu tsopano.

25Tikamasunga mokhulupirika zonse zimene Chauta Mulungu wathu watilamula, Iyeyo adzakondwera nafe.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help