Yos. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aimika miyala khumi ndi iŵiri yachikumbutso.

1Mtundu wonse wa Aisraele utaoloka Yordani, Chauta adauza Yoswa kuti,

2“Sankha amuna khumi ndi aŵiri, mmodzi pa fuko lililonse.

3Tsono uŵalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iŵiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yordanipo, pa malo amene anali kuimirira ansembewo. Nyamulani miyala imeneyo ndi kudza nayo ku zithando zanu kumene mudzagone usiku.’ ”

4Yoswa adaitana amuna khumi ndi aŵiri adaŵasankha aja,

5ndipo adaŵalamula kuti, “Loŵani mu mtsinje wa Yordaniwu patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu. Aliyense mwa inu atenge mwala pa phewa. Fuko lililonse la Aisraele litenge mwala umodzi.

6Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso, ndipo anthu azidzakumbukira zimene Chauta wachita. Ana anu akamadzakufunsani m'tsogolo muno tanthauzo lake la miyala imeneyi,

7muzidzaŵauza kuti, ‘Madzi a Yordani adaaima osayendanso, pamene Bokosi lachipangano la Chauta linkaoloka mtsinjewu.’ Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso kwa Aisraele.”

8Anthuwo adachitadi zonse zimene Yoswa adaŵalamula. Adanyamula miyala khumi ndi iŵiri pakati pa mtsinje wa Yordani, monga momwe Chauta adalamulira Yoswa. Anthu a fuko lililonse la Aisraele adanyamula mwala umodzi. Miyalayo adapita nayo kukaikhazika pansi pamalo pamene panali zithando paja.

9Yoswa adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri imene idaali pakati pa mtsinje wa Yordani, pamalo pomwe padaaimirira ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja. Miyala imeneyi ikadali kumeneko mpaka lero lino.

10Ansembe aja adaimirirabe pakati pa mtsinje wa Yordani, mpaka zitatha zonse zimene Chauta adaalamula Yoswa kuti auze anthu. Zimenezi ndizo zimene Mose anali atafotokozera Yoswa.

Tsono anthu adaoloka mtsinjewo mofulumira.

11Ansembe atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta adatsogolera anthu onse aja.

12Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la Manase, ndiwo adaoloka poyamba, ali okonzekera nkhondo, monga momwe Mose adaŵauzira.

13Asilikali ngati zikwi makumi anai adaoloka, nakaima pa tsidya, m'chigwa cha Yeriko, ali okonzekera nkhondo.

14Zimene adachita Chauta pa tsiku limenelo zidapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo adamchitira ulemu kwambiri ndi kumlemekeza monga momwe ankalemekezera Mose nthaŵi yonse ya moyo wake.

15Onse ataoloka, Chauta adauza Yoswa kuti,

16“Lamula ansembe onyamula Bokosi lachipanganowo, kuti atuluke m'madzimo.”

17Yoswa adaŵalamuladi kuti atuluke.

18Ansembewo atangoponda pa mtunda, mtsinjewo udayamba kuyendanso mpaka kumasefukira m'chibumi.

19Aisraele adaoloka mtsinje wa Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, ndipo adamanga zithando zao ku Giligala, kuvuma kwa Yeriko.

20Kumeneko ndiko kumene Yoswa adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ija imene adaaitenga ku Yordani.

21Ndipo adauza Aisraele onse aja kuti, “Ana akamadzafunsa makolo ao m'tsogolo muno kuti, ‘Kodi miyala imeneyi imatanthauzanji?’

22Inuyo muzidzaŵauza kuti, ‘Aisraele adaoloka mtsinje wa Yordaniwu pansi pali pouma.’

23Chauta, Mulungu wanu, ndiye adaaphwetsa madzi a mtsinjewo, kuti inuyo muwoloke pouma monga momwe adaaumitsira Nyanja Yofiira, mpaka tonse titaoloka.

24Chifukwa cha chimenechi, aliyense pa dziko lapansi pano adzadziŵa mphamvu za Chauta, ndipo mudzalemekeza Chauta, Mulungu wanu, mpaka muyaya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help