1Pamene Chauta anali m'chihema chamsonkhano adaitana Mose, namuuza kuti,
2“Uza Aisraele kuti, ‘Munthu aliyense akamabwera ndi chopereka kwa Chauta, azitenga ng'ombe kapena nkhosa kapena mbuzi.’
3“Ngati munthu apereka nsembe yopsereza kwathunthu, azipereka ng'ombe yamphongo yopanda chilema. Aziiperekera pa khomo la chihema chamsonkhano, kuti Chauta ailandire.
4Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake.
5Pambuyo pake aiphe pamaso pa Chauta, ndipo ansembe, ana a Aroni, abwere ndi magazi ake. Awaze magaziwo mozungulira guwa limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano.
6Ndipo asende nyamayo ndi kuidula nthulinthuli.
7Tsono ansembe, ana a Aroni aja, asonkhe moto pa guwa, ndipo ayalike nkhuni pamotopo.
8Pamenepo ansembe aike nthuli za nyamayo, mutu wake pamodzi ndi mafuta omwe, pa nkhuni zimene zili pa guwalo.
9Koma atsuke matumbo ake pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Tsono wansembe aipsereze nyama yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
10“Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya nkhosa kapena mbuzi, ikhale yaimuna yopanda chilema.
11Ndipo aiphere cha kumpoto kwa guwa, pamaso pa Chauta. Tsono ansembe, ana a Aroni, awaze magazi ake pa guwalo molizungulira.
12Pambuyo pake ataidula nthulinthuli nyamayo, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo aike zonsezo pa nkhuni zimene zili pa guwa.
13Koma matumbo ake aŵatsukire padera, pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Ndipo wansembe apereke zonsezo ndi kuzitentha pa guwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
14Ngati munthu apereka kwa Chauta nsembe yopsereza ya mbalame, ikhale njiŵa kapena nkhunda.
15Wansembe abwere nayo ku guwa, aidule mutu moipotola, ndi kutentha mutuwo paguwapo. Magazi ake aŵathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa.
16Tsono achotse chitsokomero pamodzi ndi nthenga zake zomwe, ndi kuzitaya potayira phulusa, pafupi ndi guwa, cha kuvuma kwake.
17Pambuyo pake aing'ambe pakati, phiko lina uku, lina uku, koma osachotsa mapikowo. Kenaka aitenthe pa moto wankhuni wapaguwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.