Mik. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsopano konzekani m'magulu ankhondo,

inu a ku Yerusalemu.

Atizinga ndi zithando zankhondo,

akuthira nkhondo likulu la Israele.

Za Mfumu yochokera ku Betelehemu

2 Mt. 2.6; Yoh. 7.42 Chauta akuti,

“Koma iwe Betelehemu wa ku Efurata,

inde ndiwe wamng'ono pakati pa mafuko a Yuda,

komabe mwa iwe ndidzatulutsa munthu

amene adzakhala wolamulira Israele.

Iyeyo chiyambi chake nchakalekale,

cha masiku amakedzana.”

3Nchifukwa chake Mulungu adzasiya Israele

mpaka pa nthaŵi yoti achire

mkazi amene adzabale mwana.

Pamenepo, otsala a mtundu wake

adzabwereranso kwa Aisraele anzao.

4Iye adzalimbikira, ndipo adzaŵeta nkhosa zake

mwa mphamvu za Chauta

ndi ulemerero wa dzina la Chauta,

Mulungu wake.

Ndipo iwo adzakhala mu mtendere,

poti ukulu wake udzakhazikika pa dziko lonse lapansi.

5Ndiye amene adzakhazikitse mtendere.

Aisraele apulumuka kenaka nkulangidwa

Aasiriya akadzaloŵa m'dziko mwathu

ndi kuyamba kutithira nkhondo,

tidzaŵatumira atsogoleri ankhondo asanu ndi aŵiri

kapena akalonga asanu ndi atatu.

6 Gen. 10.8-11 Iwowo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga,

dziko la Nimirodi adzalilamulira mwankhondo.

Adzatipulumutsa kwa Aasiriya,

iwowo akadzakaloŵa m'dziko mwathu,

kudzatithira nkhondo.

7Onse otsalira a Yakobe adzakhala dalitso

pakati pa mitundu yambiri ya anthu

ngati mame ochoka kwa Chauta.

Adzakhala ngati mvula yowaza pa udzu,

imene sichita kulamulidwa ndi anthu,

siidikira lamulo la munthu.

8Onse otsalira a Yakobe

adzakhala temberero

pakati pa mitundu ya anthu,

ngati mkango pakati pa nyama zam'nkhalango.

Adzakhala ngati mwana wa mkango,

pakati pa gulu la nkhosa,

amene amati akadzaziloŵerera,

amazimbwandira ndi kuzikadzula.

Ndipo sipakhala wozipulumutsa.

9Inu Aisraele, mudzapambana adani anu,

ndipo adani anu onsewo adzaonongeka.

10Komabe Chauta akuuza Aisraele kuti,

“Pa tsiku limenelo ndidzaononga akavalo anu onse,

ndipo ndidzaphwasula magaleta anu.

11Ndidzaononga mizinda ya m'dziko mwanu

ndi kugwetseratu malinga anu.

12Ndidzasakaza masenga anu onse,

ndipo pakati panu sipadzakhalanso oombeza.

13Ndidzaononga mafano anu onse

pamodzi ndi miyala yoimika

yopembedzerapo m'dziko mwanu.

Simudzazigwadiranso zinthuzo

zimene mudapanga ndi manja anu.

14Ndidzagwetsa mafano anu a Asera m'dziko mwanu,

ndipo ndidzaononga mizinda yake.

15Mwaukali ndi mokwiya

ndidzalanga mitundu yonse ya anthu

imene sidandimvere.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help