1“Upange chihema chamapemphero ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Nsalu zimenezi uzipete bwino ndi zithunzi za akerubi.
2Muutali nsalu iliyonse ikhale mamita 13, ndipo muufupi mwake ikhale pafupi mamita aŵiri. Zonsezo zikhale zofanana.
3Usoke nsalu zisanu kuti zikhale nsalu imodzi, ndipo uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.
4Upange timagonga ta nsalu yobiriŵira m'mbali mwake mwa nsalu imodzi kumapeto kwake. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu inzakeyo.
5Kenaka upange timagonga makumi asanu pa nsalu yoyambayo, ndipo timagonga tinanso makumi asanu pa nsalu yachiŵiriyo, kuti timagongato tiyang'anane.
6Tsono upange ngoŵe zagolide makumi asanu, zolumikizira nsalu ziŵirizo, kuti chipangike chihema chimodzi.
7“Uwombenso nsalu khumi ndi imodzi za ubweya wambuzi kuti zikhale lona lophimba pamwamba pa chihemacho.
8Muutali mwake nsalu iliyonse ikhale mamita 14, ndipo muufupi mwake pafupi mamita aŵiri. Zonsezo zikhale zofanana.
9Usoke nsalu zisanu kuti zikhale nsalu imodzi, ndipo zisanu ndi imodzi zinazo zikhalenso nsalu imodzi. Tsono upinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo mophatikiza patsogolo pa chihema.
10Upangenso magonga makumi asanu m'mbali mwake mwa nsalu yotsirizira ya chinsalu chimodzi, ndiponso magonga makumi asanu pa nsalu yotsiriza inayo.
11“Upange zomangira makumi asanu zamkuŵa, ndipo uziike m'magongamo. Choncho uphatikize pamodzi nsalu ziŵirizo, kuti pakhale chihema chimodzi.
12Theka la nsalu yotsalira ija idzalendeŵera kumbuyo kwa chihemacho.
13“Ndipo nsalu ya masentimita 46 yotsalira m'litali mwake pa mbali ziŵiri, izidzalendeŵera ndi kuphimba mbali ziŵirizo.
14Lona lija ulipangire chophimbira chake chofiira cha chikopa cha nkhosa zamphongo. Pambuyo pake upangenso chophimbira chotsiriza cha zikopa zofeŵa chodzayala pamwamba pa zonse.
Matabwa a chihema15“Upange mafulemu a chihemacho ndi matabwa oimirira bwino a mtengo wa kasiya.
16Muutali mwake fulemu lililonse likhale mamita anai ndi theka, ndipo muufupi mwake masentimita 69.
17Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziŵiri, ndipo mafulemu onse a chihemacho apangidwe ndi matabwa otere.
18Popanga mafulemuwo, ku mbali yakumwera, upange makumi aŵiri.
19Ndipo upange masinde makumi anai asiliva pansi pa mafulemu makumi aŵiriwo. Pansi pa fulemu lililonse pakhale masinde aŵiri ogwirizira zolumikizira ziŵiri zija.
20Ndipo kumpoto kwa chihemacho upangenso mafulemu makumi aŵiri,
21ndi masinde makumi anai asiliva, aŵiri pa fulemu lililonse.
22Kumbuyo kwake kwa chihemacho, chakuzambwe, upange mafulemu asanu ndi limodzi.
23Kumbuyo kwa chihema konko, pangodya pakhale mafulemu aŵiri.
24Mafulemu ameneŵa apangodya azilumikizidwa kuyambira pansi mpaka pa chigwinjiri chapamwamba. Umu ndimo m'mene akhalire mafulemu aŵiri amene akupanga ngodya ziŵiri.
25Motero padzakhala mafulemu asanu ndi atatu okhala ndi masinde ake 16 asiliva, aŵiri pansi pa fulemu lililonse.
26“Upange mitanda ya mtengo wa kasiya, isanu pa mafulemu a mbali ina ya chihema,
27ndi isanu inanso pa mafulemu a mbali ina. Pakhalenso mitanda isanu pa mafulemu akuzambwe chakumbuyo.
28Mtanda wa pakati penipeni pa mafulemuwo ugwire mafulemu onse, kuyambira ku mapeto mpaka ku mapeto.
29Mafulemuwo uŵakute ndi golide, ndi kulonganso mphete zagolide m'mafulemuwo kuti agwirizire mitanda ija, ndipo mitandayo ikhale yokutidwa ndi golide.
30Motero upange chihema changa monga momwe ndikukulangizira paphiri pano.
31“Usoke nsalu yotchingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Ndipo nsaluyo uipete ndi zithunzi za akerubi.
32Uikoloŵeke pa nsanamira zinai zakasiya zokutidwa ndi golide, zokhala ndi ngoŵe zagolide ndi zokhazikika pa masinde anai asiliva.
33Ahe. 6.19; 9.3-5 Ukoloŵeke nsalu yochingayo ku ngoŵezo ndipo uike bokosi lachipangano lija m'kati momwemo, kuseri kwa nsalu yochingayo. Nsalu yochingayo idzalekanitsa malo opatulika ndi malo opatulika kopambana.
34Uike chivundikiro chija pa bokosi lachipangano ku malo opatulika kopambanawo.
35Tebulo lija uliike kunja kwa nsalu yochingayo. Choikaponyale chija uchiike chakumwera kwake kwa chihemacho, mopenyana ndi tebulolo, limene likhale mbali yakumpoto.
36“Pa chipata choloŵera m'chihemamo, uikepo nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso.
37Upange nsanamira zisanu zakasiya zimene akoloŵekepo nsalu yochingayo. Zikutidwe ndi golide, ndipo ngoŵe zake zokoloŵekapo zikhalenso zagolide, ndiponso upange masinde asanu amkuŵa a nsanamira zimenezo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.