Ezek. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yolirira Tiro

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, uimbe nyimbo yodandaulira Tiro.

3Uuze Tiro, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, umene umachita malonda ndi anthu a mitundu yambiri ya ku maiko ambiri a m'mbali mwa nyanja, kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi:

“ ‘Iwe Tiro, wakhala ukunena kuti,

“Ndine wokongola kwabasi.”

4Malire ako ali m'kati mwenimweni mwa nyanja.

Amisiri amene adakumanga,

adakumanga ngati chombo chochititsa kaso zedi.

5Adakupanga ndi matabwa

a mitengo ya paini ya ku phiri la Seniri.

Adatenga mkungudza ku Lebanoni

kuti adzapangire mlongoti wako.

6Adapanga nkhafi zako

ndi mtengo wa thundu wa ku Basani.

Adapanga thandala lako

ndi matabwa a mitengo ya paini ya ku zilumba za Kitimu,

pakati pa matabwawo panali zosema za minyanga ya njovu.

7Thanga lako linali la nsalu yabafuta.

Nsalu yake inali yopeta bwino, yochokera ku Ejipito,

ndipo ndiyo inali ngati mbendera yako.

Nsalu zophimba mahema ako

zinali zobiriŵira ndi zofiirira,

zochokera ku zilumba za Elisa.

8Anthu a ku Sidoni ndi a ku Arivadi

ndiwo amene ankakupalasa.

Akatswiri ako, iwe Tiro, anali mwa iwe,

ndiwo amene ankakuyendetsa.

9Mwa iwe munalinso akuluakulu ndi akatswiri a ku Gebala,

amene ankakonza ziboo zako.

Amalinyero ambiri m'zombo zao ankadzakuyendera

kuchokera ku maiko onse

kudzachita nawe malonda.’

10“Anthu a ku Persiya, a ku Ludi ndi a ku Puti adaloŵa m'gulu la ankhondo ako. Ankapachika zishango zao ndi zisoti m'kati mwako, ndipo potero ankakupatsa ulemerero.

11Ankhondo a ku Arivadi ndi a ku Heleki ankalonda malinga ako ponse pozungulira. Anthu a ku Gamadi ankakwera pa nsanja zako, ndi kukapachika zishango zao pa malinga ako ponse pozungulira. Amenewo ndiwo amene ankakukongoletsa kwabasi.

12“Dziko la Tarisisi linkachita nawe malonda chifukwa cha katundu wako wamtundumtundu, ndipo unkagulako siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu, mosinthana ndi katundu wako.

13Yavani, Tuba ndi Meseki ankachita nawe malonda. Ankakugulitsa akapolo ndi ziŵiya zamkuŵa mosinthana ndi katundu wako.

14Anthu a ku Betetogarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthana ndi katundu wako.

15Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, anthunso a m'mbali mwa nyanja ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo mosinthana ndi katundu wako.

16Anthu a ku Aramu ankagula zinthu zambiri zamalonda mosinthana ndi katundu wako wochuluka. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korale ndi miyala ya rubi, mosinthana ndi katundu wako.

17Yuda ndi Israele ankagula malonda ako. Iwo ankapereka tirigu, zipatso za olivi, nkhuyu zoyamba, ndiponso uchi, mafuta aolivi ndi zonunkhira zokometsera chakudya, mosinthana ndi katundu wako.

18Anthu a ku Damasiko ankagula kwa iwe chifukwa cha kuchuluka kwa zamalonda zako ndi katundu wako wosiyanasiyana. Ankakugulitsa vinyo wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wambee.

19Ankaperekanso vinyo wa ku Uzala, ndiponso zitsulo zosalala, kasiya ndi bango lonunkhira, kusinthitsa ndi malonda ako.

20Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoika pa zishalo za akavalo.

21Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara ankachita nawe malonda mosinthana ndi ana a nkhosa, nkhosa zamphongo ndi mbuzi.

22Amalonda a ku Sheba ndi a ku Rama ankagulanso kwa iwe. Ankapereka zonunkhira zabwino kwambiri, miyala ya mtengo wapatali ndi golide yemwe, mosinthana ndi katundu wako.

23Mizinda iyi ya Harani, Kane, Edeni, Asuri ndi Kilimade inkachita nawe malonda.

24Anthu akumeneko ankasinthitsana nawe zovala zabwino kwambiri, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, makalipeti amaŵangamaŵanga, zonsezo atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.

25Chiv. 18.11-19 Zombo za ku Tarisisi zinkanyamula malonda ako.

“Motero iweyo unali ngati chombo chapanyanja

chodzaza ndi katundu wolemera.

26Opalasa ako adakupititsa ku nyanja yozama,

kumene mphepo yakuvuma idakukankhira

nikumiza m'kati mwa nyanja.

27Chuma chako, katundu wako ndi malonda ako,

amalinyero ako ndi oongolera omwe,

amisiri a matabwa a zombo zako

ndiponso oyendetsa malonda ako,

asilikali ako onse amene anali m'katimo,

ndi gulu lonse lankhondo pakati pako,

onsewo adamira m'nyanja tsiku limene udaonongeka.

28Chifukwa cha kufuula kwa amalinyerowo,

kumtunda kudagwedezeka.

29Onse amene amapalasa chombo,

atuluka m'zombo zao.

Amalinyero onse ndi oongolera omwe aimirira ku mtunda.

30Onsewo akukulira iweyo,

kulira kwake kwambiri.

Akudzithira fumbi kumutu,

nkumamvimvinizika pa phulusa.

31Akudzimeta mpala chifukwa cha iwe,

ndipo akuvala ziguduli.

Akulira ndi mitima yoŵaŵa.

32Akukuimbira nyimbo yodandaula,

akuti, ‘Ndani adaonongedwapo ngati Tiro,

pakati pa nyanja?’

33Pamene malonda ako ankaoloka nyanja,

unkakondweretsa mitundu yambiri ya anthu pa zosoŵa zao.

Mafumu a dziko lapansi adalemera nacho chuma chako.

34Koma tsopano wathyokera m'nyanja,

pansi penipeni pa nyanja.

Kungoti iweyo, katundu wako ndi antchito ako onse,

nonse mwathera pamodzi m'nyanja.

35Aliyense amene amakhala m'mbali mwa nyanja

waopsedwa nazo zimene zakuchitikira.

Mafumu ao akuchita mantha,

nkhope zao zasinthika ndi mantha.

36Anthu amalonda a ku maiko ena akukunyodola tsopano.

Watha mochititsa mantha,

sudzakhalaponso mpaka muyaya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help