1Pambuyo pake Nahasi, mfumu ya Aamoni, adamwalira, ndipo Hanuni, mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
2Tsono Davide adati, “Ine ndidzamchitira zabwino Hanuni mwana wa Nahasi, pakuti inenso bambo wake ankandichitira zabwino.” Choncho Davide adatuma amithenga kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika kwa Hanuni, m'dziko la Aamoni, kuti akampepese.
3Koma akalonga a Aamoni adauza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide watuma anthu odzakuthuzitsani mtima, ndiye kuti akulemekeza bambo wanu? Osati atumiki akewo abwera kwa inu kuti adzazinde dziko, ndipo kuti akalipenya, alilande?”
4Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adadula zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao.
5Tsono Davide adamva za atumiki akewo, adatuma anthu kuti akakumane nawo, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye mudzabwere kuno.”
6Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, Hanuni ndi Aamoniwo adatumiza siliva wa makilogramu 34,000, kuti akalipirire magaleta ndiponso anthu a pa akavalo a ku Mesopotamiya, a ku Aramaaka ndi a ku Zoba.
7Adalipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi gulu lake lankhondo. Amenewo adabwera nadzamanga zithando zankhondo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni adabwera kuchokera ku mizinda yao kudzamenya nkhondo.
8Davide atamva zimenezo, adatuma Yowabu pamodzi ndi gulu lake lonse la ankhondo.
9Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa chipata cha mzinda. Koma mafumu amene adaadzawo anali paokha ku malo opanda mitengo.
10Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo.
11Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni.
12Tsono Yowabu adauza Abisai kuti, “Ngati Asiriya andipose mphamvu, iwe udzandithandize. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ineyo ndidzabwera kudzakuthandiza.
13Khala wolimba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”
14Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriyawo kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika.
15Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, mbale wa Yowabu, nakaloŵa mu mzinda. Pamenepo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu.
16Koma Asiriya ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adatuma amithenga kuti abwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate, pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.
17Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani nkukaŵapeza Asiriyawo. Adandanditsa ankhondo ake kuti amenyane nawo. Tsono pamene Davide ankandanditsa ankhondo ake mopenyana ndi Asiriya, iwoŵa adayamba kumenyana naye.
18Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo ankhondo a Davide adapha Asiriya okwera magaleta ankhondo okwanira 7,000, ndi ankhondo apansi okwanira 40,000. Adaphanso Sofaki mtsogoleri wa gulu lao lankhondo.
19Tsono akalonga a Hadadezere ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adapangana za mtendere ndi Davide, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya sadafunenso kumathandiza Aamoniwo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.