1Pali zinthu zitatu zimene zimasangalatsa
mtima wanga,
zimenenso zimakondweretsa Mulungu ndi anthu onse.
Zinthu zake ndi izi: chiyanjano pakati pa abale,
chibwenzi pakati pa anthu oyandikana,
ndipo mwamuna ndi mkazi okhalitsana bwino.
2Pali anthu a mitundu itatu amene ndimadana nawo
amene moyo wao umandinyansa kwambiri.
Anthu ake ndi aŵa:
munthu wosauka amene ali wonyada,
munthu wolemera amene ali wonama,
ndipo nkhalamba yokonda zigololo imene ilibe nzeru.
3Ngati sudapeze kanthu ukali mwana,
kodi ungapate kanthu bwanji utakalamba?
4Kuganiza mwanzeru kumaŵakhala bwino anthu aimvi,
ndipo kulangiza ena bwino kumazikhala bwino nkhalamba.
5Nzeru zimaŵakhaladi bwino anthu okalamba
ndipo khalidwe lakumvetsa ndi lauphungu
limaŵayenerera akuluakulu olemekezeka.
6Ulemerero wa munthu wokalamba wagona pa
kudziŵa zinthu zambiri,
ndipo chimene amanyadira nkuwopa Ambuye.
7Pali zinthu zisanu ndi zinai zondisangalatsa mtima,
palinso china chakhumi chimene ndichita kunena:
munthu wonyadira ana ake,
munthu wotha kuwona kugwa kwa adani ake iye akali moyo.
8Ngwodala mwamuna amene ali ndi mkazi wanzeru,
ngwodala mlimi amene saphatikiza ng'ombe ndi
bulu polima ndi pulao,
ngwodala munthu amene sanachimwepo polankhula,
ngwodalanso munthu amene sadagwirire ntchito
munthu woluluka koposa iye.
9Ngwodala munthu amene ali ndi nzeru zabwino,
munthu woti akalankhula anzake amatchera khutu.
10Ngwamkuludi munthu amene wapeza nzeru,
komabe munthu woopa Ambuye palibe amene angampose.
11Kuwopa Ambuye kumapambana zonse.
Kodi munthu woopa Ambuye tingamfanizire ndi yani?
12Kuwopa Ambuye ndiye chiyambi cha kuŵakonda Ambuyewo,
ndipo chikhulupiriro ndiye chiyambi cha
kuphathikana nawo.
Za mkazi woipa13Bala lililonse chabwino, koma osati bala lokhala mu mtima.
Njiru iliyonse chabwino, koma osati njiru ya munthu wamkazi.
14Vuto lililonse chabwino, koma osati vuto lochokera
kwa odana nawe.
Kulipsira kulikonse chabwino, koma osati kulipsira kwa mdani.
15Palibe ululu woopsa kupambana wa njoka,
ndipo palibe mkwiyo woopsa kupambana mkwiyo wa mdani.
16Ndi bwino kukhala pamodzi ndi mkango kapena chinjoka,
kupambana kukhala pamodzi ndi mkazi woipa.
17Mkazi akakwiya,
maonekedwe ake amasinthika,
nkhope yake imaoneka ngati
ya chimbalangondo chaukali.
18Mwamuna wake amapita kukadya nawo kwa anzake,
sangaleke kudandaula kwambiri.
19Choipa china chilichonse si kanthu,
kuyerekeza ndi njira ya mkazi.
Tsoka la anthu ochimwa ligwere mkaziyo.
20Monga momwe imavutikira nkhalamba pokwera
phiri lamchenga,
ndi m'menenso amavutikira mwamuna wofatsa
ndi mkazi wolongolola.
21Usatengeke naye mtima mkazi wokongola,
ndipo usakhumbire mkazi wachuma.
22Ngati ndi mkazi amene akupeza ndalama zofunikira pa banja,
zotsatira zake ndi mkwiyo, kulongolola ndiponso manyazi aakulu.
23Manyazi, nkhope yotsika, ndi kupwetekedwa mtima
ndizo zimene amabweretsa mkazi wanjiru.
Manja aulesi ndi maondo olobodoka, ndizo zimene
amabweretsa mkazi wosasangalatsa mwamuna wake.
24Tchimo lidayamba ndi munthu wamkazi.
Ngati tonsefe timafa, nchifukwa cha iyeyo.
25Usalole madzi kutayikira pa mng'alu.
Usalolenso mkazi woipa kumalankhula mwamwano.
26Ngati sachita zinthu
monga m'mene ukulamulira iweyo, usiyane naye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.