1 Am. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Pa nthaŵi imeneyo wansembe wina dzina lake Matatiasi, mwana wa Yohane, mdzukulu wa Simeoni, wansembe wa m'banja la Yowaribu, adachoka ku Yerusalemu, nakakhala ku Modini.

2Matatiasi anali ndi ana aamuna asanu. Maina ao naŵa: Yohane wotchedwa Gadisi,

3Simoni wotchedwa Tasi,

4Yudasi wotchedwa Makabeo,

5Eleazara wotchedwa Avarano, ndi Yonatani wotchedwa Afusi.

6Matatiasi adaona zoipa za kunyoza Mulungu zimene zinkachitika ku Yuda ndi ku Yerusalemu.

7Ndipo adati,

“Kalanga ine! Ndidabadwiranji

kuti ndiwone kutha kwa mtundu wanga

ndi kwa mzinda woyera?

Kodi ine ndizingokhala khale,

pamene mzinda waperekedwa kwa adani,

ndipo Nyumba ya Mulungu ili m'manja mwa

anthu achilendo?

8Nyumba ya Mulungu yasanduka ngati munthu

wotha ulemu.

9Ziŵiya zake zonyaditsa adazitenga ngati

zofunkha.

Makanda ake adaŵakantha m'miseu yake.

Anyamata ake adaphedwa ndi adani pa nkhondo.

10Kodi ulipo mtundu wa anthu

umene sudalandeko chigawo cha ufumu wake

ndi kufunkha katundu wake?

11Adauchotsera makaka ake onse.

Udaali mfulu, koma wasanduka kapolo.

12Nyumba yopembedzeramo Mulungu,

yokongola kwambiri ndi yaulemerero ija,

yasanduka bwinja,

anthu a mitundu ina adaiipitsa.

13Nanga ifeyo tikhalirenjinso ndi moyo?”

14Tsono Matatiasi ndi ana ake adang'amba zovala zao navala chiguduli, ndipo adalira kwambiri.

15Tsiku lina asilikali a mfumu okakamiza anthu kuti aleke chipembedzo chao, adadza ku Modini kuti aumirize anthu kupereka nsembe.

16Aisraele ambiri adakasonkhana nao, koma Matatiasi ndi ana ake adaima pa okha.

17Asilikali a mfumu Antioko adauza Matatiasi kuti, “Iwe ndiwe mtsogoleri ndiponso munthu womveka ndi wamphamvu mu mzinda uno, ndipo ana ako ndi abale ako ali pambuyo pako.

18Uyambe ndi iweyo kutsata lamulo la mfumu, monga momwe achitira anthu a mitundu inamu, monganso achitira atsogoleri a ku Yuda omwe pamodzi ndi anthu otsala ku Yerusalemu. Choncho iwe ndi ana ako mudzakhala abwenzi a mfumu. Adzakulemekezani nkukupatsani golide, siliva ndi mphatso zina zambiri.”

19Pa zimenezi Matatiasi adayankha ndi mau okweza kuti, “Ngakhale anthu a mitundu ina yonse, okhala mu ulamuliro wa mfumu, amamumvera ndi kusiya chipembedzo cha makolo ao, ndi kutsata malamulo ake,

20ine ndekha, ana anga ndi abale anga, tidzasunga chipangano cha makolo athu.

21Atithandize Mulungu kuti tisaleke kutsata Malamulo ake.

22Sitidzamvera kulamula kwa mfumu. Sitidzapatuka pa chipembedzo chathu, kuloŵera kumanja kapena kumanzere.”

23Atatha kulankhulaku, Myuda wina adadzaima patsogolo, anthu onse akupenya, kuti apereke nsembe pa guwa la ku Modini, pofuna kutsata lamulo la mfumu.

24Matatiasi atampenya adapsa mtima zedi, nayamba kunjenjemera ndi ukali. Adamlumphira munthuyo ndi mkwiyo wachilungamo, namuphera paguwa pomwepo.

25Nthaŵi yomweyo adaphanso nduna ya mfumu imene inkaumiriza anthu kupereka nsembe, kenaka nkuligamula guwalo.

26Num. 25.6-15Motero changu cha Matatiasi chokonda Malamulo chidamchititsa zimenezo, monga muja adaachitira Finehasi, kupha Zimuri, mwana wa Salu.

Matatiasi amenya nkhondo

27Pambuyo pake Matatiasi adalengeza mumzindamo mokweza mau kuti, “Aliyense wotsimikiza kusunga Chipangano ndi Malamulo abwere anditsate.”

28Tsono iye ndi ana ake adathaŵira ku mapiri, nkusiya zonse zimene anali nazo mumzindamo.

29Pa nthaŵi imeneyo Ayuda ambiri ofuna kusunga chipembedzo chao ndi chilungamo, nawonso adakakhala ku chipululu.

30Adapita ndi ana ao, akazi ao, ndi ziŵeto zao, chifukwa mavuto ao anali ochuluka.

31Mbiri ya zimenezi idafika kwa atsogoleri ankhondo a mfumu ndi kwa gulu lankhondo lokhala ku Yerusalemu, mzinda wa Davide. Adamva kuti anthu ena amene adakana malamulo a mfumu, apita ku chipululu kukabisala.

322Am. 6.11Pomwepo ankhondo ambiri adanyamuka mofulumira nkuŵalondola. Ataŵapeza, adamanga zithando zankhondo mopenyana nawo, nakonzekera kumenyana nawo nkhondo pa tsiku la Sabata.

33Adaŵafuulira kuti, “Nthaŵi ikalipo, tulukani, mumvere malamulo a mfumu, ndipo mudzakhala ndi moyo.”

34Ayuda aja adayankha kuti, “Iyai, ife sitituluka, sitidzatsata malamulo a mfumu kapena kuipitsa tsiku la Sabata.”

35Pompo asilikaliwo adayambapo nkhondo.

36Koma Aisraele sadaŵabwezere, sadaŵaponye miyala, ndipo sadatseke pa mapanga ao.

37Adangonena kuti, “Ife tonse mutipha popanda chifukwa, tilibe cholakwa chilichonse, kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni.”

38Tsono iwo aja adaŵathira nkhondo tsiku la Sabata, naŵapha iwowo, akazi ao, ana ao ndi ziŵeto zao zomwe. Anthuwo anali okwanira chikwi chimodzi.

39Matatiasi ndi abwenzi ake atamva zimenezo, adaŵalira kwambiri.

40Adauzana kuti, “Ife tikachita zonga zimene adachita abale athuŵa, tikapanda kumenyana nawo nkhondo anthu a mitundu inaŵa kuti tisunge moyo wathu ndi malamulo athu ndi mwambo wathu, ndiye kuti adzatiwononga tonse pa dziko lapansi.”

41Tsono tsikulo adamvana kuti, “Munthu aliyense akadzayambana nafe nkhondo ngakhale pa tsiku la Sabata, tidzamenyane naye, tisafe tonse monga m'mene adafera abale athu m'mapanga muja.”

42Anthu a m'banja la Asidea adaphatikana nawo. Anali Aisraele olimba mtima ndi ofuna kuteteza Malamulo.

43Onse othaŵa mavuto adadzaphatikana nawo, nkuchulukitsa gulu lao.

44Atasonkhanitsa khamu lao lankhondo, adakantha anzao ochimwawo mwachipseramtima, nakanthanso mwaukali amene adaasiya chipembedzo chao. Amene adapulumukapo adathaŵira kwa anthu a mitundu ina.

45Matatiasi pamodzi ndi abwenzi ake adayendera dziko, kuti agumule maguwa onse achikunja.

46Adaumbala ana onse amene adaŵapeza ali osaumbalidwa m'dziko la Israele.

47Adapirikitsa adani ao achipongwe, nakhozadi pa ntchito zaozo.

48Adateteza Malamulo aja kuti asanyozedwe ndi anthu a mitundu ina ndi mafumu aja, ndipo sadalole kuti anthu onyoza Malamulowo apambane.

Matatiasi alangiza ana ake pakufa

49Matatiasi ali pafupi kufa, adauza ana ake kuti, “Mwano ndi chipongwe zikukulirakulira, nthaŵi ino ndi yamavuto ndi ya mkwiyo waukali.

50Tsono inu ana anga, onetsani changu chanu chotsata Malamulo, mupereke moyo wanu chifukwa cha chipangano cha makolo athu.

51Kumbukirani ntchito zimene makolo anu adazichita pa mibadwo yao, ndipo mudzaona ulemu waukulu ndi mbiri yosatha.

52Gen. 15.6; 22.15-18Kodi suja Abrahamu adapezeka kuti ngwokhulupirika pamene ankayesedwa? Kodi suja adapezeka wolungama chifukwa cha kumvera kwake?

53Gen. 39.1—45.28Yosefe, nthaŵi ya mavuto ake, adatsata Malamulo, nasanduka mkulu woyang'anira Ejipito.

54Finehasi kholo lathu, adalandira lonjezo la unsembe wosatha, chifukwa cha chikondi chake choyaka chokonda za Mulungu.

55Num. 13.1—14.12Yoswa, popeza kuti adaasenza ntchito yake mpaka kuitsiriza, adasanduka woweruza Aisraele.

56Kalebe adalandira chigawo chakechake cha dziko, chifukwa adaachita umboni woona pa msonkhano.

572Sam. 7.16Davide, chifukwa cha kukhulupirika kosagwedezeka, adalandira mpando wa ufumu wamuyaya.

582Maf. 2.9-12Eliya, chifukwa chokhala ndi changu chachikulu chotsata Malamulo, adakwezedwa kumwamba.

59Dan. 3.8-30Hananiya, Azariya ndi Misaele adapulumuka m'ng'anjo yamoto, chifukwa cha kukhulupirira Mulungu.

60Dan. 6.1-24; Bel. 1.31-42Daniele anali wa mtima wangwiro, nchifukwa chake adapulumuka kukamwa kwa mikango.

61“Tsono muzindikire kuti mu mbadwo uliwonse, anthu onse okhulupirira Mulungu sadzafooka konse.

62Musaope mau a munthu woipa uja, chifukwa ulemu wake upita ku ndoŵe ndi ku mphutsi.

63Lero adzikuza, maŵa lino osaonekanso, chifukwa wabwerera ku fumbi, ndipo zolinga zake zatheratu.

64Tsono inu ana anga, mukhale amphamvu ndi olimba mtima potsata Malamulo, motero mudzapeza ulemerero.

65“Onani Simoni mbale wanu. Ndikudziŵa kuti iye uja ndi munthu wanzeru polangiza ena. Muzimumvera nthaŵi zonse, ndipo adzakhala ngati bambo wanu.

66Yudasi Makabeo ndi munthu wolimba mtima kuyambira pa unyamata wake. Iyeyo akhale mtsogoleri wa gulu lanu lankhondo, azidzamenyana nkhondo ndi anthu a mitundu ina.

67Muphatikane nawo onse otsata Malamulo, ndipo muŵalipsire onse ovutitsa mtundu wanu.

68Muŵabwezere akunja zomwe adakuchitani, ndipo muchite khama kusunga Malamulo.”

69Atatero, Matatiasi adadalitsa ana ake, kenaka nkufa.

70Adamwalira chaka cha 146. Tsono ana ake adamuika m'manda a makolo ake ku Modini. Aisraele adalira maliro ake ndi chisoni chachikulu.

Yudasi Makabeo
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help