Mas. 107 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kutamanda ubwino wa Mulungu

1 1Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11 Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

pakuti chikondi chake nchamuyaya.

2Anenedi choncho oomboledwa a Chauta,

amene Iye waŵapulumutsa ku mavuto.

3Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse,

kuchokera kuvuma ndi kuzambwe,

kumpoto ndi kumwera.

4Ena adasokera m'chipululu,

osapeza njira yopita ku mzinda woti akakhalemo.

5Adamva njala ndi ludzu,

moyo wao unkafookeratu.

6Tsono anthu aja adalira kwa Chauta

pamene anali m'mavuto amenewo,

ndipo Chauta adaŵapulumutsa.

7Adaŵatsogolera pa njira yolunjika

mpaka anthuwo adakafika ku mzinda woti akakhalemo uja.

8Athokoze Chauta

chifukwa cha chikondi chake chosasinthika,

chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.

9Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu,

amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.

10Ena adakhala mu mdima ali ndi chisoni,

anali am'ndende ozunzika m'maunyolo achitsulo,

11pakuti adaatsutsa mau a Mulungu,

adaakana monyoza malangizo a Wopambanazonse.

12Iye adaŵapsinja ndi ntchito yakalavulagaga,

motero iwo adagwa pansi, popanda mmodzi woŵathandiza.

13Tsono anthu aja adalira kwa Chauta

pamene anali m'mavuto amenewo,

ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo.

14Chauta adaŵatulutsa anthuwo mu mdima

ndi m'chisoni muja,

ndipo adadula maunyolo ao.

15Athokoze Chauta

chifukwa cha chikondi chake chosasinthika,

chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.

16Pajatu adathyola zitseko zamkuŵa,

nadula paŵiri mipiringidzo yachitsulo.

17Ena adadwala chifukwa cha njira zao zoipa,

nazunzika chifukwa cha machimo ao.

18Sankafuna chakudya cha mtundu uliwonse,

ndipo adayandikira ku zipata za imfa.

19Tsono anthu aja adalira kwa Chauta

pamene anali m'mavuto amenewo,

ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo.

20Chauta adatumiza mau ake, naŵachiritsa anthuwo,

adaŵapulumutsa kuti asaonongeke.

21Athokoze Chauta

chifukwa cha chikondi chake chosasinthika,

chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.

22Apereke nsembe zothokozera,

ndi kulalika ntchito za Chauta,

poimba nyimbo zachimwemwe.

23Ena adakayenda ku nyanja m'zombo,

namachita malonda pa Nyanja yaikulu.

24Adaona ntchito za Chauta,

ntchito zake zodabwitsa, pa madzi akuya.

25Ndiye kuti Chauta adalamula

nautsa namondwe amene adaŵindula mafunde apanyanja.

26Zombozo zidakwera mpaka m'mwamba

nkutsikiranso kwakuya,

ndipo anthuwo adataya mtima pa mavuto aowo.

27Adachita chizungulire

namadzandira ngati anthu oledzera,

kenaka nkuthedwa nzeru.

28Tsono anthu aja adalira kwa Chauta

pamene anali m'mavuto amenewo,

ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo.

29Chauta adatontholetsa namondwe,

ndipo mafunde apanyanja adachita bata.

30Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata,

ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.

31Athokoze Chauta

chifukwa cha chikondi chake chosasinthika,

chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.

32Amtamande pa msonkhano wa anthu,

amuyamike pa bwalo la akuluakulu.

33Adasandutsa mitsinje kuti ikhale chipululu,

adasandutsa akasupe a madzi kuti akhale nthaka youma,

34 Mphu. 39.23 dziko lachonde adalisandutsa nthaka yamchere,

chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala m'menemo.

35Komanso adasandutsa chipululu

kuti chikhale ndi maiŵe a madzi,

nthaka youma kuti ikhale akasupe a madzi.

36Ndipo kumeneko Chauta adakhazikako anthu anjala,

tsono anthuwo adamanga mzinda woti azikhalamo.

37Adafesa mbeu m'minda, namaoka mipesa,

ndipo adakolola dzinthu dzambiri.

38Chifukwa cha madalitso a Chauta,

anthuwo adachuluka kwambiri,

Chauta sadalole kuti zoŵeta za anthuwo zichepe.

39Pamene anthu ake chiŵerengero chao chidachepa,

ndipo pamene adatsitsidwa

chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni,

40apo Chauta adagwetsa manyozo pa mafumu oŵapsinja

naŵasokeretsa, m'chipululu.

41Koma anthu osoŵa adaŵatulutsa m'mavuto ao,

adachulukitsa mabanja ao ngati magulu a nkhosa.

42Anthu olungama mtima amaona zimenezo, nkumasangalala,

koma oipa onse amaŵakhalitsa chete.

43Munthu aliyense wanzeru asamale zimenezi,

anthu alingalire za chikondi chosasinthika cha Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help