1Ndidzaimba nyimbo
zotamanda kukhulupirika ndi kulungama.
Ndidzakuimbirani Inu Chauta.
2Ndidzatsata njira yopanda cholakwa.
Nanga mudzabwera liti kwa ine?
Ndidzakhala ndi mtima wangwiro m'nyumba mwanga.
3Sindidzaika maso anga
pa chinthu chilichonse chachabechabe.
Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani,
sizindikomera konse.
4Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa,
sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine.
5Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa.
Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.
6Koma anthu okhulupirika am'dziko,
ndidzaŵayang'ana moŵakomera mtima,
ndipo adzakhala ndi ine.
Oyenda m'njira yopanda cholakwa adzanditumikira.
7Palibe munthu wochita zonyenga
amene adzakhale m'nyumba mwanga.
Palibe munthu wolankhula zabodza
amene adzakhale pafupi ndi ine.
8Tsiku ndi tsiku ndidzaononga oipa onse am'dziko.
Onse ochita zoipa ndidzaŵachotsa mu mzinda wa Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.