Yon. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero la Yona

1Tsono Yona ali m'mimba mwa chinsomba chija,

adayamba kutama Chauta mopemba.

2Adati,

“Inu Chauta, pamene ndinali m'mavuto ndidakuitanani,

ndipo mudandiyankha.

Pamene ndinali m'dziko la akufa

ndidalira kwa Inu kuti mundithandize,

ndipo mudamva pempho langa.

3Mudandiponya m'nyanja yozama,

m'kati mwenimweni mwa njanja,

ndipo mweza wam'nyanjamo udandizungulira.

4Pamene ndidati,

‘Mwanditaya kutali ndi Inu.

Kodi ndidzaiyang'ananso bwanji Nyumba yanu yoyera?’

5Madzi adandiyesa m'khosi,

nyanja yozama idandizungulira.

Udzu wakayandeyande udandikwidzinga m'mutu.

6Ndidatsikira kunsi ndithu, m'tsinde mwa mapiri,

kudziko kumene mipiringidzo idanditsekera mpaka muyaya.

Koma Inu Chauta, Mulungu wanga,

mudanditulutsa kumandako ndili moyo.

7Poona kuti ine nkufatu kuno,

ndidakumbukira Inu Chauta,

pemphero langa lidakufikani m'Nyumba yanu yoyera.

8Anthu opembedza milungu yachabe

amataya kukhulupirika kwao.

9Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu

ndi mau okuthokozani.

Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu.

Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”

10Apo Chauta adalamula chinsomba chija kuti chisanzire Yona ku mtunda.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help