1Ha! Achikhala unali mlongo wanga,
woyamwa bere limodzi ndi ine!
Ndikadakumana nawe panjira,
bwenzi ntakumpsompsona,
ndipo wina aliyense sakadandinyoza.
2Ndikadakutenga
nkukuloŵetsa m'nyumba ya amai anga,
m'chipinda cha amene adandibala.
Ndikadakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe,
ndi madzi a makangaza.
3Ine ndikadatsamira dzanja lako lamanzere,
iwe nkundikumbatira ndi dzanja lamanja.
4Inu akazi a ku Yerusalemu,
ndithu ndakupembani,
chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa
mpaka pamene chifunire ichocho.
Nyimbo Yachisanu ndi chimodziAkazi
5Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo,
atatsamira wokondedwa wake?
Mkazi
Ndidakudzutsa patsinde pa mtengo wa apulosi uja.
Pamenepo mpamene amai ako adachirira pokubala iweyo.
6Umatirire mtima wako
kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha,
ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha.
Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa,
nsanje njaliwuma ngati manda.
Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi
ngati malaŵi a moto,
ndipo nchotentha koopsa.
7Ngakhale madzi ochuluka sangachizimitse chikondi,
ngakhale madzi a chigumula sangachikokolole.
Ngakhale munthu atapereka chuma chonse cha m'nyumba
chifukwa chofuna kugula chikondi,
adzangonyozeka nazo kotheratu.
Alongo a Mkazi
8Tili naye ife mlongo wathu wamng'ono,
alibe ndi maŵere omwe.
Tidzamchitira chiyani mlongo wathu
pa tsiku limene adzamfunsire mbeta?
9Iye akakhala ngati khoma,
tidzammangira nsanja yasiliva.
Koma akakhala ngati chitseko,
tidzamchinga ndi matabwa amkungudza.
Mkazi
10Ine ndili ngati khoma,
ndipo maŵere anga ali ngati nsanja zake.
Tsono m'maso mwa wokondedwa wanga
ndili ngati wodzetsa mtendere.
Mwamuna
11Solomoni anali ndi munda wamphesa ku Baala-Hamoni.
Mundawo adaubwereka alimi.
Aliyense mwa iwo ankayenera kupereka
ndalama zasiliva chikwi chimodzi kuti azilimamo.
12Koma munda wanga wamphesa ndi wangawanga,
ndiponso wa ine ndekha.
Iwe Solomoni, khala nazo ndalama chikwi chimodzi zija,
khala nawonso alimi ako mazana aŵiri aja.
13Iwe amene umakhala m'munda
anzanga akumvetsera kuti amve liwu lako.
Tandilola kuti ndilimve.
Mkazi
14Fulumiratu wokondedwa wanga,
khala ngati mphoyo
kapena ngati mwanawambaŵala wothamanga m'mapiri,
m'mene mumamera mbeu zokometsera chakudya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.