Mas. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizoKwa Woimbitsa Nyimbo. Aimbire zeze.Salmo la Davide.

1Thandizeni, Inu Chauta,

palibenso munthu wosamala za Inu,

okhulupirika sapezekanso pakati pa anthu.

2Aliyense amangonamiza mnzake,

amathyasika ndi pakamwa pake,

amalankhula ndi mitima iŵiri.

3Inu Chauta, tsekani pakamwa ponse pothyasika

letsani lilime lililonse lolankhula modzikuza.

4Paja anthu amenewo amanena kuti,

“Tidzapambana ndi mau athu,

pakamwa tili napo, nanga angatigonjetse ndani?”

5Chifukwa choti osauka alandidwa zao

ndipo osoŵa akudandaula,

Chauta akunena kuti,

“Ndichitapo kanthu tsopano,

ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.”

6Malonjezo a Chauta ndi angwiro,

ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto,

woyeretsedwa kasanunkaŵiri.

7Titetezeni, Inu Chauta,

titchinjirizeni nthaŵi zonse kwa anthu ameneŵa,

8pakuti anthu oipa amangoyendayenda ponseponse,

ndipo anzao amayamikira zochita zao zoipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help