Mas. 109 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Dandaulo la munthu amene ali pa mavutoKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Musakhale chete, Inu Mulungu,

amene ndimakutamandani,

2pakuti anthu oipa ndi onama amakamba zondiwukira,

amalankhula zondinamizira.

3Ponseponse amandilankhula mau achidani,

amandinena popanda chifukwa.

4M'malo mwa chikondi changa,

iwo amandibwezera zondineneza,

ngakhale pamene ndikuŵapempherera.

5Motero amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino,

amandiwonetsa chidani m'malo mwa chikondi changa.

6Sankhulani munthu woipa

kuti aweruze mlandu wa wondiwukirayo,

iye aimbidwe mlandu ndi munthu woneneza anzake.

7Pomuweruza apezeke kuti ali ndi mlandu,

mapemphero ake akhale ngati kupalamula.

8 Ntc. 1.20 Masiku ake akhale oŵerengeka,

wina alandire udindo wake.

9Ana ake akhale amasiye,

ndipo mkazi wake akhale mfedwa.

10Ana ake azingoyendayenda nkumapemphapempha,

apirikitsidwe m'mabwinja m'mene amakhala.

11Wokongoza ndalama amlande zonse zimene ali nazo.

Alendo afunkhe zimene adapindula ndi ntchito yake.

12Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima,

kapena wina woŵachitira chifundo

ana ake amasiye aja.

13Zidzukulu zake zithe nkufa,

dzina lao lisamvekenso mu mbadwo wachiŵiri.

14Chauta asaiŵale machimo a makolo ake,

machimo a mai wake asafafanizike.

15Chauta asakhululukire machimowo mpaka muyaya,

anthuwo aiŵalike pa dziko lapansi.

16Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo,

koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima,

mpaka kuŵapha.

17Ankakonda kutemberera,

choncho matemberero amgwere.

Sadakonde kudalitsa anthu ena,

choncho madalitso akhale kutali ndi iye.

18Kutemberera anzake kunali ngati chovala chake,

motero matemberero amgwere ngati mvula.

Akhale ngati mafuta oloŵa m'mafupa mwake.

19Matemberero akhale ngati mwinjiro wofundira,

ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.

20Zimenezi zikhale chilango

chochokera kwa Chauta kugwera ondineneza.

Ziŵagwere amene amalankhula zoipira moyo wanga.

21Koma Inu Mulungu, Ambuye anga,

munditchinjirize

malinga ndi ulemerero wa dzina lanu,

mundipulumutse

chifukwa chikondi chanu chosasinthika ndi chabwino.

22Pakuti ine ndine wosauka ndi wosoŵa,

ndipo mtima wanga ukuŵaŵa kwambiri.

23Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo,

ndapirikitsidwa ngati dzombe.

24Maondo anga afooka chifukwa chosala zakudya,

thupi langa laonda ndi mutu womwe.

25 Mt. 27.39; Mk. 15.29 Ondineneza amandinyodola,

akandiwona amapukusa mitu yao.

26Thandizeni Chauta, Mulungu wanga.

Pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

27Adani adziŵe

kuti limeneli ndi dzanja lanu londipulumutsa,

Inu Chauta, ndinu amene mwachita zimenezi.

28Iwo atemberere, koma Inu mundidalitse.

Ondiputa muŵachititse manyazi,

koma ine mtumiki wanu ndisangalale.

29Ondineneza akhale onyozeka,

manyazi ao aŵakute ngati chovala.

30Ndidzathokoza Chauta kwambiri polankhula.

Ndidzamtamanda pakati pa gulu la anthu.

31Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa,

amafuna kumpulumutsa kwa anthu

ogamula kuti iyeyo aphedwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help