Eks. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mose alengeza za imfa ya ana achisamba

1Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tsopano ndimlanga kamodzi kokha Farao, pamodzi ndi Aejipito onse. Pambuyo pa chilango chimenechi, adzakulolani kuti muchoke. Zoonadi, akadzakulolani kuti muchoke, adzachita chokupirikitsani kuno.

2Tsopano lankhula ndi anthu, ndipo uuze mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense, kuti apemphe zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide kwa Mwejipito aliyense woyandikana naye.”

3Ndipo Chauta adafeŵetsa Aejipito kuti akomere Aisraele mtima. Chinanso nkuti Mose anali wotchuka kwambiri m'dziko la Ejipito, pamaso pa nduna za Farao ndiponso pamaso pa anthu onse.

4Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Ndiyenda pakati pa Aejipito pakati pa usiku,

5ndipo mwana aliyense wachisamba adzaphedwa mu Ejipito monse muno. Kuyambira mwana wachisamba wa Farao, amene ali woyenera kuloŵa ufumu, adzaphedwa, mpaka mwana wachisamba wa mdzakazi amene akupera pa mphero. Mwana woyamba kubadwa wa zoŵeta adzafanso.

6M'dziko lonse la Ejipito mudzakhala maliro okhaokha amene sadaonekepo nkale lonse, ndipo sadzaonekanso.

7Koma pakati pa Aisraele, ndi galu yemwe sadzauwa munthu kapena choŵeta chilichonse, kuti mudziŵe kuti Chauta amasiyanitsa Aejipito ndi Aisraele.

8Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine kudzandigwadira, zidzati, “Chokani inu pamodzi ndi anthu anu onse!” Tsono pambuyo pake, ndidzachoka.’ ” Mose adachoka kwa Farao kuja mokwiya kwambiri.

9Chauta adauza Mose kuti, “Farao sadzakumvera iwe, kuti pakutero, Ine ndichite zozizwitsa m'dziko la Ejipito.”

10Motero Mose ndi Aroni adachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao. Koma Chauta adamuumitsa mtima Faraoyo, ndipo Aisraelewo sadaŵalole kuti achoke m'dziko mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help