1 Afi. 3.5 Tsono ndikufunsa kuti, “Kodi Mulungu adataya anthu ake?” Iyai, chosatheka! Inenso ndine Mwisraele, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini.
2Mulungu sadaŵataye anthu ake amene Iye adaŵasankha kale. Monga simudziŵa mau aja a m'Malembo, pamene mneneri Eliya akudandaula kwa Mulungu kuti aŵalange Aisraele? Paja adati,
31Maf. 19.10, 14 “Ambuye, anthu ameneŵa adapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha, ndipo akufuna kupha ndi ine ndemwe.”
41Maf. 19.18 Koma Mulungu adamuyankha chiyani? Adati, “Ndadzisungira anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri amene sadapembedzepo Baala, mulungu wonama uja.”
5Tsono ndi momwemonso makono. Patsala Aisraele oŵerengeka amene Mulungu adaŵasankha mwa kukoma mtima kwake.
6Komatu ngati adaŵasankha chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye kuti si chifukwa cha zimene iwo adaachita. Zikadatero, kukoma mtima kwake sikukadakhalanso kukoma mtima ai.
7Bwanji tsono? Aisraele sadapeze zimene ankafunafuna. Koma anthu pang'ono chabe amene Mulungu adaŵasankha ndiwo adazipeza. Otsalawo adagontha m'khutu,
8Deut. 29.4; Yes. 29.10 monga Malembo anenera kuti,
“Mulungu adaŵapatsa mtima wosatha kumvetsa zinthu,
ndipo mpaka lero lino waŵasandutsa osatha kupenya
ndi osatha kumva.”
9 Mas. 69.22, 23 Ndipo Davide akuti,
“Maphwando ao asanduke msampha ndi diŵa loŵakola,
ndi kuŵagwetsa kuti alangidwe.
10Maso ao atsekedwe kuti asapenye,
ndipo msana wao ukhale wopindika nthaŵi zonse.”
Za chipulumutso cha anthu a mitundu ina11Tsono ndikufunsa kuti, “Kodi Ayuda adaphunthwa kuti agweretu osadzukanso?” Mpang'ono pomwe. Koma chifukwa cha kuchimwa kwa Ayudawo, chipulumutso chidafikiranso anthu a mitundu ina, kuti Ayuda aŵachitire nsanje.
12Ngati kuchimwa kwa Ayuda kudapindulitsa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo ngati kulephera kwao kudapindulitsa kwakukulu anthu a mitundu ina, nanji tsono onse akadzamvera Mulungu, ndiye kuti madalitso adzakula zedi.
13Tsopano ndifuna kukuuzani kanthu, inu amene simuli Ayuda. Malinga nkuti ndine wotumidwa kwa anthu a mitundu ina, ndimaunyadira utumiki wanga umenewu.
14Koma ndimakhumba kuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena mwa iwo.
15Ngati anthu a pa dziko lonse lapansi adayanjanitsidwa ndi Mulungu chifukwa Iye adaŵaika pambali Ayuda, nanga kudzatani Iye akadzaŵalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka!
16Ngati munthu apatulira Mulungu chigawo chimodzi cha buledi, ndiye kuti yenseyo ndi wopatulika. Ndipo ngati muzu wa mtengo ndi wopatulika, ndiye kuti ndi nthambi zake zomwe nzopatulika.
17Nthambi zina za mtengo wobzala wa olivi zidakadzuka, ndipo pamalo pa nthambi zimenezo adalumikizapo kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo. Ndiye kuti inu amene simuli Ayuda, muli ngati kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo uja, ndipo tsopano mukulandira nao mphamvu ya m'mizu ya mtengo wobzala wa olivi, ndiye kuti Ayuda.
18Nchifukwa chake musamaŵanyoze amene adakadzuka monga nthambi zija. Kodi inu mungadzitame bwanji? Inutu ndinu kanthambi chabe. Sindinu amene mumagwirizira muzu ai, koma muzu ndiwo umene umagwirizira inu.
19Tsono mudzati, “Koma nthambi zija zidakadzuka kuti andilumikizepo ineyo pamtengopo.”
20Nzoona, iwo adakadzukadi chifukwa sadakhulupirire, ndipo inu pakukhulupirira, mukukhala mu mtengo tsopano. Komatu tsono musamadzitame, makamaka muzichita mantha.
21Mulungu sadaŵalekerere Ayuda, amene ali ngati nthambi zenizeni za mtengo. Kodi tsono mukuyesa kuti adzakulekererani inuyo?
22Pamenepo zindikirani kuti Mulungu ndi wachifundodi, komanso ndi waukali. Kwa anthu amene adagwa, ndi wokwiya, koma kwa inu ndi wachifundo, malinga mukasamala chifundo chake. Ngati simuchita zimenezi, adzakudulani inunso.
23Ndipo ngati enawo aleka kusakhulupirira kwao, adzaŵalumikizanso ku mtengo. Pakuti Mulungu ndi wamphamvu, atha kuŵalumikizanso.
24Inu, amene muli nthambi ya mtengo wa olivi wakuthengo, Mulungu adakukadzulani ku mtengo umene udaakubalani, nakulumikizani ku mtengo wa olivi wobzala. Ngati zili choncho, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuti alumikizenso ku mtengo wa olivi wobzala, nthambi zakezake zimene zidakadzuka?
Chifundo cha Mulungu pa anthu onse25Pali chinsinsi, chimene ndifuna kuti muchidziŵe, kuwopa kuti mungamadziyese anzeru. Chinsinsicho ndi chakuti Aisraele ena adzapulupudza, mpaka nthaŵi imene chiŵerengero cha akunja otembenukira kwa Mulungu chidzakwanire.
26Yes. 59.20, 21 Pamenepo Aisraele onse adzapulumuka. Ndi monga Malembo anenera kuti,
“Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni,
adzachotsera zidzukulu za Yakobe kuipa kwao konse.
27 Yes. 27.9 Ndidzapangana nawo chipangano chimenechi
ndikadzaŵachotsera machimo ao.”
28Chifukwa chokana Uthenga Wabwino, Ayuda asanduka adani a Mulungu, kuti inu mupindulepo. Koma ngati Mulungu adaŵasankha, iwo ndi abwenzi ake chifukwa cha makolo ao akale aja.
29Pakuti Mulungu sasinthanso ataitana munthu ndi kumpatsa mphatso.
30Kale inu a mitundu ina simunkamvera Mulungu, koma tsopano Mulungu akukuchitirani chifundo chifukwa cha kusamvera kwa Ayuda.
31Momwemonso Ayuda tsopano samvera Mulungu, koma cholinga chake nchakuti iwonso adzalandire chifundo pa nthaŵi yake, chifukwa cha chifundo mwalandira inuchi.
32Mulungu adasandutsa anthu onse akaidi a kusamvera, kuti Iye athe kuchitira onse chifundo.
Mulungu ndi wolemekezeka33 Yes. 55.8; Lun. 17.1 Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
34Yes. 40.13Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti,
“Ndani amadziŵa maganizo a Chauta,
ndani angamupatse malangizo?
35 Yob. 41.11 Ndani adaayamba waperekapo kanthu kwa Mulungu,
kuti Mulunguyo amubwezereko kanthu?”
36 1Ako. 8.6 Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.