Yes. 41 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu alimbitsa Israele mtima

1Mulungu akuti,

“Mukhale chete ndipo mundimvere,

inu maiko a m'mphepete mwa nyanja.

Anthu a mitundu yonse akhale

ndi mphamvu zatsopano.

Asendere ndi kulankhulapo.

Tiyeni tikhale pamodzi pa mlandu atiweruze.

2“Kodi ndani adabweretsa

wogonjetsa uja wochokera kuvuma,

wonka napambana kulikonse kumene amapita?

Ndani amamthandiza kuti apambane

anthu a mitundu ina, ndi kugonjetsa mafumu?

Lupanga lake limaŵasandutsa anthuwo

kukhala ngati fumbi lapansi,

uta wake umaŵamwaza ngati mankhusu.

3Amaŵalondola namayenda mosavutika,

m'njira zimene mapazi ake sadayendemo kale.

4Ndani adachita zimenezi mpaka kuzitsiriza,

osakhala amene adayambitsa mitundu yonse ya anthu?

Ndi Ineyo, Chauta, amene ndine chiyambi,

ndipo ndidzakhalabe yemweyo pakati pa otsiriza.”

5Anthu a maiko a m'mphepete mwa nyanja

aona zimene ndachita ndipo aopsedwa,

anthu a pa mathero a dziko lapansi ali njenjenje.

Akusendera pafupi, akubwera.

6Aliyense akuthandiza mnzake,

akuuza mbale wake kuti, “Limba mtima.”

7Mmisiri wa matabwa

amalimbikitsa mmisiri wosungunula golide,

wosalaza fano ndi nyundo

amalimbikitsa wolisanja pa chipala,

ndipo ponena za kuwotcherera amati,

“Kwachitika bwino.”

Kenaka amalikhomerera fanolo ndi misomali

kuti lisagwedezeke.

8 2Mbi. 20.7; Yak. 2.23 Koma iwe Israele mtumiki wanga,

iweyo Yakobe amene ndakusankhula,

ndiwe mdzukulu wa Abrahamu bwenzi langa.

9Ndidakutenga kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,

ndidakuitana kuchokera ku mbali zakutali za dziko.

Ndipo ndidzakuuza kuti,

“Iwe ndiwe mtumiki wanga,

ndidakusankhula, sindidakutaye.”

10Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe,

usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako.

Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza,

ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

11Motero onse amene akukupsera mtima

adzachita manyazi ndi kunyazitsidwa.

Amene akumenyana nawe

adzakhala ngati salinso kanthu,

ndipo adzafa.

12Udzafunafuna amene amakangana nawe, koma osaŵapeza.

Amene amamenyana nawe nkhondo

adzakhala ngati salinso kanthu.

13Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja,

ndine amene ndikukuuza kuti,

“Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”

14Usaope, iwe Yakobe, wofooka ngati nyongolotsi,

usachite mantha, iwe Israele, wooneka ngati mtembo,

chifukwa Ineyo ndidzakuthandiza.

Mpulumutsi wako ndine, Woyera uja wa Israele.

15Ndidzakusandutsa ngati

chipangizo chopunthira tirigu,

chatsopano, cha mano akuthwa.

Udzanyenya mapiri ndi kuŵaphwanyaphwanya.

Magomo udzaŵasandutsa mankhusu.

16Udzaŵapeta, ndipo adzauluka

ndi mphepo nadzamwazika ndi namondwe.

Koma iwe udzakondwa chifukwa

choti Ine ndine Mulungu wako.

Udzapeza ulemerero chifukwa

cha Ine, Woyera uja wa Israele.

17Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi,

koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao

kwangoti gwa ndi ludzu,

Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao,

Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya.

18Ndidzayendetsa mitsinje pakati pa zitunda zouma,

ndipo akasupe adzatumphuka m'zigwa.

Ndidzasandutsa chipululu kukhala chidziŵe cha madzi,

ndi dziko louma kukhala akasupe.

19M'chipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya,

mchisu ndi mtengo wa olivi.

M'dziko louma ndidzabzala mitengo

ya paini ya mitundu itatu.

20Choncho anthu adzaona ndi kudziŵa,

adzazindikira ndi kumvetsa

kuti Chauta ndiye adachita zimenezi,

kuti Woyera uja wa Israele ndiye adakonza zimenezi.

Chauta anyodola milungu yonama

21Chauta akuuza milungu kuti,

“Dzafotokozeni mlandu wanu.”

Chauta, Mfumu ya Yakobe akuti,

“Perekani umboni wanu.

22Mubwere kuno, mudzatiwuze zam'tsogolo.

Mufotokozere bwalo zamakedzana,

kuti tiziganizire,

ndipo tidziŵe zotsatira zake,

kapena mutiwuze zakutsogolo.

23Tiwuzenitu zimene zidzachitike

kutsogolo kuti tidziŵe kuti ndinu milungudi.

Chitani zabwino kapena kubweretsa masoka,

kuti mutidabwitse ndi kutichititsa mantha.

24Inuyo sindinu kanthu konse,

ndipo zochita zanu nzopandapake.

Amene amakupembedzaniyo amandinyansa.

25“Ndautsa munthu wina kumpoto, ndipo wabwera.

Munthuyo, kuchokera chakuvuma,

amamva kuitana pomutchula dzina.

Amaponda olamulira ngati matope,

monga m'mene munthu woumba mbiya amapondera mtapo.

26Ndani adaululiratu zimenezi poyamba pomwe

kuti ife tidziŵe?

Ndani adatiwuziratu zimenezi zisanachitike,

kuti ife tinene kuti, ‘Wakhoza?’

Palibe ndi mmodzi yemwe adazinena,

palibe ndi mmodzi yemwe adazilengeza,

ndipo palibe amene adamva mau anu.

27Ine Chauta ndine amene

ndidayambirira kumuuza Ziyoni kuti,

‘Si awo! Akubwera!’

Ndine amene ndidatuma munthu wokanena

uthenga wabwinowu ku Yerusalemu.

28Koma ndikayang'ana, palibe ndi mmodzi yemwe:

palibe wotha kulangiza,

palibe wotha kuyankha mafunso anga.

29Ndithudi, milungu yonseyi njachabe,

zochita zake si kanthu konse.

Mafano ake osungunula ali ngati mphepo yachabechabe.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help