1Chauta akunena kuti,
“Fuula kwambiri, usaleke,
mau ako amveke ngati lipenga.
Uŵauze anthu anga za kulakwa kwao,
uŵauze a m'fuko la Yakobe za machimo ao.
2Masiku onse iwo amaoneka ngati
akufuna kuchita zimene Ine ndifuna.
Amangonena kuti afuna kumvera malamulo a Mulungu wao.
Amandipempha kuti ndigamule mlandu wao mwachilungamo,
ndipo amakondwera kukhala pafupi ndi Mulungu wao.”
3Anthu akufunsa kuti,
“Kodi tizisaliranji zakudya,
pamene Inu Chauta simulabadako?
Kodi tivutikirenji nkudzichepetsa,
pamene Inu simusamalako?”
Chauta akunena kuti,
“Kunena zoona,
tsiku limene mumasala zakudya lija,
mumafunafuna zimene zingakupatseni phindu,
mumazunza antchito anu onse.
4Mumati uku mukusala zakudya,
uku mukukangana ndi kumenyana,
mpaka kutchayana ndi nkhonya zopwetekana.
Kodi mukuyesa kuti Ine nkumvera mapemphero anu,
chifukwa cha kusala zakudya kotereku.
5Kodi kusala kumene ndimafuna Ine nkumeneku,
kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?
Inu mumaŵerama pansi ngati udzu,
mumayala ziguduli nkuthirapo phulusa kuti mugonepo.
Kodi ndiye mumati kusala kumeneku,
tsiku lokondwetsa Chauta?
6“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku:
masulani maunyolo ozunzira anzanu,
masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera.
Opsinjidwa muŵapatse ufulu,
muthetse ukapolo uliwonse.
7 Mt. 25.34 Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu,
osoŵa pokhala muziŵapatsako malo.
Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala,
musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
8“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha,
ndipo mabala anu adzapola msanga.
Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani,
ndipo ulemerero wanga
udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
9“Mukamapemphera ndidzakumverani,
ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani.
Mukaleka kuzunza anzanu,
mukasiya kulozana chala,
mukaleka kunena zoipa za anzanu,
10mukamadyetsa anthu anjala,
ndi kuthandiza anthu ozunzika,
ndiye kuti mdima wokuzingani
udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
11Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse,
ndi kukupatsani zabwino.
Matupi anu ndidzaŵalimbitsa.
Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri,
ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
12Anthu anu adzamanganso nyumba
zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali.
Adzamanganso pa maziko akalekale.
Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma,
omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.”
Mphotho ya kulemekeza tsiku la Sabata13Chauta akunena kuti,
“Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata,
osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera.
Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa,
tsiku loyera la Chauta
muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka.
Muzililemekeza pakusayendayenda,
poleka kugwira ntchito zanu
ndiponso posakamba nkhani zachabe.
14Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta,
ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani
pa dziko lonse lapansi.
Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu.
Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.