Num. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ntchito za ansembe ndi za Alevi

1Pambuyo pake Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe pamodzi ndi ana ako ndi banja la makolo ako pamodzi nawe, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza malo opatulika kwambiri. Ndipo iwe ndi ana ako, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza unsembe.

2Ubwere nawonso abale ako a fuko la Levi, fuko la kholo lako, kuti azigwira nawe ntchito, azikuthandiza iwe pamodzi ndi ana ako, pamene mukutumikira m'chihema chaumboni.

3Iwowo adzakutumikirani ndi kugwiranso ntchito zonse zam'chihema. Koma asadzafike pafupi ndi zipangizo za m'malo opatulika kapena guwa, kuti iwowo pamodzi ndi inuyo mungafe.

4Iwo adzagwira nawe ntchito, ndi kumatumikiranso m'chihema chamsonkhano pa ntchito zonse zam'chihemamo. Ndipo wina aliyense asadzafike pafupi ndi inu.

5Mudzatumikira pa ntchito za m'malo opatulika ndi pa ntchito za guwa, kuti mkwiyo usaŵagwerenso Aisraele.

6Ndaŵasankha abale ako, Alevi, pakati pa Aisraele. Iwowo ndi mphatso kwa iwe, aperekedwa kwa Chauta kuti azitumikira m'chihema chamsonkhano.

7Tsono iwe pamodzi ndi ana ako, muzitumikira pa ntchito zaunsembe, ntchito zonse zokhudza guwa, ndi pa ntchito zonse za m'malo opatulika kwambiri. Ndakupatsa unsembe ngati mphatso yako, koma munthu wina aliyense wofika pafupi, adzaphedwa.”

Gawo la ansembe

8Chauta adauzanso Aroni kuti, “Pa zopereka kwa Ine, ndakupatsa zotsala zimene amasunga, ndiye kuti zinthu zimene Aisraele amapatulira Ine. Ndakupatsa zimenezi kuti zikhale gawo lako ndi la ana ako, kuti zikhale zanu mpaka muyaya.

9Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako.

10Muzidyera ku malo opatulika kopambana. Mwamuna aliyense angathe kudyako. Zimenezi nzoyera kwa inu.

11Zinanso zanu ndi izi: zopereka zao zamphatso, ndi zopereka zoweyula za Aisraele. Zimenezi ndazipereka kwa iwe, kwa ana ako aamuna, ndi kwa ana ako aakazi amene ali ndi iwe, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Munthu aliyense amene ali wosaipitsidwa angathe kudyako.

12Ndakupatsani mafuta onse abwino kopambana, vinyo yense ndi mbeu zonse zabwino kwabasi, ndi zipatso zonse zoyamba zimene anthu amapereka kwa Chauta.

13Mwa zinthu zonse za m'dziko mwako, zipatso zoyambirira kupsa zimene amapereka kwa Chauta, zimenezo zikhale zanu. Munthu aliyense wosaipitsidwa m'nyumba mwanu angathe kudyako.

14Lev. 27.28 Chinthu chilichonse chimene anthu amapatulira Chauta m'dziko la Israele chikhale chanu.

15Chinthu chilichonse choyamba kubadwa, kaya ndi munthu kaya nyama, chimene amapereka kwa Chauta, chikhale chanu, Komabe mwana wamwamuna wachisamba muzimuwombola, ndiponso pakati pa nyama zosayenera kuzipereka ku nsembe, mwana wake woyamba kubadwa muzimuwombola.

16(Muzimuwombola akakhala wa mwezi umodzi). Uike mtengo wake woombolera kuti ukhale ndalama zisanu zasiliva, molingana ndi ndalama za ku malo opatulika.

17Koma mwanawang'ombe woyamba kubadwa kapena mwanawankhosa woyamba kubadwa, kapenanso mwanawambuzi woyamba kubadwa, musaŵaombole. Amenewo ngoyera. Muwaze magazi ao pa guwa, ndipo mutenthe mafuta ao kuti akhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.

18Koma nyama yake ikhale yako, monga momwe imakhalira nganga yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja.

19Zopereka zonse zoyera zimene Aisraele amapereka kwa Chauta ndakupatsa iwe, ana ako aamuna ndi ana ako aakazi ali ndi iwe. Zimenezi zikhale zako mpaka muyaya. Chimenechi ndicho chipangano chamuyaya pamaso pa Chauta, chochita ndi iwe ndi ana ako.”

20Ndipo Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe udzakhala wopanda choloŵa m'dziko mwao, ndiponso udzakhala wopanda gawo lililonse pakati pao. Ine ndine gawo lako ndi choloŵa chako pakati pa Aisraele.

Gawo la Alevi

21 Lev. 27.30-33; Deut. 14.22-29 “Ndaŵapatsa Alevi chachikhumi chilichonse m'dziko la Israele kuti chikhale chigawo chao, chifukwa cha ntchito imene akuigwira m'chihema chamsonkhano.

22Kuyambira tsopano Aisraele asamafika pafupi ndi chihema chamsonkhano, kuti angachimwe ndipo angafe.

23Koma Alevi ndiwo amene azitumikira m'chihema chamsonkhano, ndipo adzalangidwa ngati alakwa pa udindo wao. Limeneli likhale lamulo pa mibadwo yanu yonse. Aleviwo asakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.

24Tsono chachikhumi chimene Aisraele amapereka kwa Chauta, ndapatsa Aleviwo kuti chikhale chigawo chao. Nchifukwa chake ndaŵauza kuti asadzakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.”

Chachikhumi cha Alevi

25Chauta adauza Mose kuti,

26“Uŵauzenso Alevi kuti, ‘Pamene mulandira kwa Aisraele chachikhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale chigawo chanu, muperekeko chachikhumi cha chachikhumicho kuti chikhale nsembe kwa Chauta.

27Ndipo chopereka chanucho chidzaŵerengedwa ngati tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya.

28Choncho inunso muzipereka zopereka zanu kwa Chauta, zotapa pa chachikhumi chilichonse chimene mulandira kwa Aisraele. Pa zimene mwalandirazo mutengeko mphatso ya Chauta, ndipo mupatse wansembe Aroni.

29Pa mphatso zonse zimene mwalandira, mupatuleko zake za Chauta, ndipo zimene mwapatulazo zikhale zabwino kopambana zina zonse.’

30Nchifukwa chake uŵauze kuti, ‘Mutaperekako zabwino kopambana zina zonse, zotsalazo muziŵerengere kuti nzanu, monga tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya.

31Mungathe kuzidyera pa malo aliwonse, inuyo ndi a m'banja mwanu. Zimenezo ndi mphotho yanu chifukwa cha ntchito imene mumagwira m'chihema chamsonkhano.

32Ndipo simudzachimwa mukadya zimenezo, ngati mwapereka kale kwa Chauta zabwino kopambana zina zonse. Motero simudzanyoza zinthu zoyera za Aisraele ndipo simudzafa.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help