Ezek. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ezekiele aneneratu za nkhondo ya ku Yerusalemu

1Mulungu adati, “Iwe mwana wa munthu, tenga phale, uliike pamaso pako, ndipo ulembepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu.

2Mzindawo uuzinge ndi ngalande, uunde mitumbira yankhondo, uuzinge ndi zithando zankhondo ndipo uzike makina ogumulira, kuzungulira mzindawo.

3Utenge chitsulo, uchiimike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyang'anitsitse mzindawo, ndipo uumangire zithando zankhondo ndi kuuzinga kotheratu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraele.”

4“Tsono ugonere kumanzere kwako, ndipo machimo a anthu a ku Israele ndidzaŵaika pa iwe. Udzasenza machimo aowo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo.

5Ndachitatu kukuikira masiku, okwanira 390, kulinganiza ndi zaka za machimo ao. Umu ndimo m'mene udzasenzere machimo a Aisraele.

6Utatha zimenezi, udzatembenuke nkugonera ku dzanja lamanja. Tsono udzasenze machimo a anthu a ku Yuda pa masiku makumi anai, tsiku lililonse kulinganiza ndi chaka chathunthu cha chilango chao.

7Uyang'anitsitse zithando zankhondo zozinga Yerusalemu. Ukwinye dzanja la mkanjo wako, ukweze mkono wako ndipo ulose modzudzula Yerusalemu.

8Ndithudi, ndidzakumanga ndi zingwe, kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku, mpaka kuzingidwa kwa Yerusalemu kutatha.

9“Tsopano tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mcheŵere, zonsezo uziike m'mbale imodzi, kenaka upange buledi. Uzidzadya pa masiku 390 amene udzakhale ukugonera mbali imodzi.

10Udzayeseko theka la kilogramu la bulediyo, kuti akhale chakudya chako. Uzidzadya kamodzi kokha pa tsiku.

11Uyesekonso makapu aŵiri a madzi, kuti akhale chakumwa chako cha tsiku ndi tsiku.

12Udzadya buledi wako wophika ngati makeke abarele. Ndoŵe youma ya anthu ndiyo idzakhale nkhuni zako zophikira, ndipo uzidzaphikira kumene anthu angathe kukuwona.”

13Tsono Chauta adati, “Buledi ameneyu ndiye chifaniziro cha chakudya chodetsedwa chimene Aisraele azidzadya ku maiko achilendo kumene ndidzaŵapirikitsire.”

14Koma ine ndidati “Inu Ambuye Chauta, inetu sindidadziipitsepo motero pa chipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka lero lino, sindidadyepo nyama yofa yokha kapena yojiwa ndi zilombo, ndipo sindidadyepo nyama yonyansa pa zachipembedzo.”

15Apo Iye adati, “Chabwino, ndidzakulola kuphikira ndoŵe ya ng'ombe m'malo mwa ndoŵe ya anthu, pophika buledi.”

16Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzaŵachepetsera buledi wa tsiku ndi tsiku. Anthuwo buledi wao azidzachita woyesa, ndipo azidzadya mwankhaŵa. Madzi aonso azidzachita oyesa, nkumamwa mwamantha.

17Motero chakudya ndi madzi zidzaŵathera pang'onopang'ono. Azidzada nkhaŵa akamapenyana, ndipo adzatheratu nkuwonda chifukwa cha machimo ao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help