Eks. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chauta adauza Mose kuti, “Taona, ndidzakusandutsa kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mbale wako Aroni ndiye adzakhale ngati mneneri wako.

2Zonse zimene ndakulamulazi ukazinene, ndipo iye ndiye akauze Farao kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.

3Ntc. 7.36 Komatu ndidzamuumitsa mtima, ndipo ngakhale ndidzachite zozizwitsa zambiri ndi zodabwitsa ku Ejipito,

4Faraoyo sadzakumverani. Pamenepo ndidzakantha dzikolo, ndipo pochita ntchito zamphamvu, ndidzatsogolera magulu anga, anthu anga Aisraele, kuŵatulutsa ku Ejipito.

5Apo Aejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵakantha ndi dzanja langa ndi kutulutsa Aisraele m'dziko mwaomo.”

6Ndipo Mose ndi Aroni adachitadi zomwe Chauta adaŵalamulazo.

7Pamenepo nkuti Mose ali wa zaka 80 ndipo Aroni wa zaka 83, pa nthaŵi imene ankalankhula ndi Farao.

Ndodo ya Aroni

8Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,

9“Ngati Farao akulamulani kuti, ‘Chitani chozizwitsa kuti tikukhulupirireni,’ iwe Mose ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao kuti isanduke njoka.’ ”

10Choncho Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adaponya pansi ndodo yake ija pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo idasanduka njoka.

11Zitatero Farao adaitana anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo iwowo adachitanso zomwezo mwa matsenga ao.

12Adaponyanso pansi ndodo zao, ndipo zidasanduka njoka. Koma ndodo ya Aroni ija idameza ndodo zaozo.

13Farao adaumabe mtima, ndipo sadasamale zimene ankamuuzazo monga momwe Chauta adaanenera muja.

Zoopsa zigwera Ejipito: Madzi asanduka magazi

14 Lun. 11.6-8 Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Farao ndi wokanika kwambiri, akukana kulola anthu anga kuti apite.

15Upite m'maŵa ukakumane naye pamene akupita ku mtsinje wa Nailo. Ukamdikire pambali pa mtsinjewo. Tsono utenge ndodo ija idaasanduka njokayi.

16Ukamuuze Farao kuti Chauta, Mulungu wa Ahebri, wandituma kwa inu kuti ndikuuzeni mau aŵa: ‘Uŵalole anthu anga apite, akandipembedze ku chipululu. Koma mpaka tsopano lino sudandimverebe.’

17Chiv. 16.4 Zimene Chauta akunena ndi izi, akuti ‘Poona zimene ndichite, udzadziŵa kuti Ine ndinedi Chauta. Taona, ndidzamenya madzi a mu mtsinjewu ndi ndodo ili m'manja mwangayi, ndipo madzi onseŵa adzasanduka magazi.

18Nsomba zonse zidzafa, ndipo madziwo adzanunkha, kotere kuti Aejipito sadzafunanso kumwa madzi a mu mtsinje umenewu.’ ”

19Chauta adalamulanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, uilozetse ku madzi onse mu Ejipito muno, monga mitsinje, ngalande ndiponso zithaphwi ndi maiŵe omwe. Madziwo adzasanduka magazi, ndipo m'dziko monsemo mudzakhala magazi okhaokha, ngakhale m'zotungira madzi zomwe, zamitengo ndi zamiyala.’ ”

20Motero Mose ndi Aroni adachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adasamula ndodo yake namenya madzi amumtsinje pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo madzi onsewo adasanduka magazi.

21Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito.

22Tsono amatsenga a ku Ejipito aja nawonso adachita zomwezo mwa matsenga ao, ndipo Farao adakhalabe wokanika. Sadamvere zimene ankanena Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.

23Pompo Farao adapotoloka, napita kunyumba kwake osalabadanso zimenezo.

24Aejipito onse adayamba kukumba m'mbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sankathanso kumwa madzi a mu mtsinjewo.

25Padapita masiku asanu ndi aŵiri, Chauta ataipitsa mtsinje uja.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help