Tob. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tobiti alangiza mwana wake

1Tsiku limenelo, Tobiti adakumbukira ndalama zimene adaasungiza Gabaele ku Ragesi, ku Mediya.

2Mumtima mwake adati, “Paja ndapempha kuti ndife, bwanji ndiitane mwana wanga Tobiyasi ndi kumdziŵitsa za ndalamazi ndisanafe.”

3Tsono adaitana Tobiyasi mwana wake, ndipo iye atabwera, Tobiti adamuuza kuti, “Ndikadzafa, udzandiike mwaulemu. Uzilemekeza amai ako, ndipo usadzaŵasiye ndi tsiku limodzi lomwe pa nthaŵi ya moyo wao. Uzidzachita zoŵakomera, ndipo usadzavutitse konse moyo wao.

4Mwana wanga, uziŵakumbukiradi amai ako, pakuti adaona zoopsa zambiri chifukwa cha iwe m'mene unali m'mimba mwao. Akadzafa, udzaŵaike pafupi ndi ine, m'manda amodzi.

5“Mwana wanga, masiku onse uzikumbukira Ambuye, Mulungu wathu, ulewe machimo, ndipo usamaphwanye Malamulo ake. Uzigwira ntchito zabwino masiku onse a moyo wako, ndipo usamayenda m'njira zosalungama.

6Dziŵa kuti ukamachita zokhulupirika, udzakhoza pa ntchito zako. Ndipo zidzateronso kwa onse otsata zolungama.

7 Deut. 15.7, 8; Miy. 19.17; Mphu. 3.30—4.6; 1Yoh. 3.17 “Anthu osauka uziŵagaŵirako chuma chako, ndipo mtima wako usamanyinyirika poŵapatsapo. Mnzako aliyense wosauka usamfulatire, ndipo Mulungu nawenso sadzakufulatira.

8Uzigaŵa zinthu malinga ndi m'mene chiliri chuma chako. Ngati uli ndi zinthu zambiri uzipatsako zambiri, ngati uli ndi zinthu zochepa usaope kuŵagaŵirako pang'ono ponse.

9Paja kupatsa nkuikiza, nkudziikira chuma kukonzekera tsiku la mavuto.

10Kupatsako kumapulumutsa ku imfa, ndipo kumatchinjiriza munthu kuti asaloŵe mu mdima.

11Kupatsa kotero kumakomeradi Mulungu Wopambanazonse.

12“Mwana wanga, bwino nawo akazi achiwerewere. Usankhule mkazi wa m'banja la makolo ako. Usakwatire mkazi wachilendo amene sali wa fuko la bambo wako, chifukwa ife ndife ana a aneneri. Kumbukira Nowa, Abrahamu, Isaki, makolo athu akale. Onsewo adakwatira akazi a mtundu wao, ndipo Mulungu adaŵadalitsa poŵapatsa ana, motero zidzukulu zao zidzakhala eniake a dziko lapansi.

13Iwenso mwana wanga, uzikonda abale ako. Usanyoze abale ako, ana aamuna ndi aakazi a mtundu wako, ndipo udzasankhule mkazi wako pakati pa iwo. Paja kunyada kumadzetsa chiwonongeko chachikulu ndi mavuto ambiri. Ulesinso umadzetsa manyazi ndi umphaŵi, ulesiwo ndiye mai wa njala.

14“Malipiro a munthu aliyense wokugwirira ntchito uzimpatsa tsiku lomwelo. Ukatumikira Mulungu, iwenso udzalandira malipiro. Mwana wanga, uzigwira mwanzeru ntchito zako zonse, ndipo makhalidwe ako onse akhale abwino pa moyo wako wonse.

15Mt. 7.12; Lk. 6.31Usachitire mnzako zomwe iwe umadana nazo. Usamwe vinyo mpaka kuledzera. Kumwa kwauchidakwa kusasanduke khalidwe.

16“Anjala uŵapatse chakudya, ndipo ausiŵa uŵapatse zovala. Ngati zinthu zakuchulukira, uthandizeko osauka, ndipo mtima wako usanyinyirike poŵathandiza.

17Deut. 26.14Pereka mwaufulu buledi ndi vinyo wako pa maliro a anthu olungama, koma pa maliro a anthu ochimwa usaperekepo kanthu ai.

18“Uzipempha nzeru kwa munthu aliyense waluntha, ndipo usamanyoza malangizo oyenera kukuthandiza. Pa zonse uziyamika Ambuye Mulungu.

19Uziŵapemphera kuti njira zako zikhale zolungama, ndiponso kuti zonse zimene uzilinga ndi kuzichita zidzakupindulire. Nzeru zotere sizipezeka kwa anthu a mitundu ina iliyonse. Koma Ambuye ndiwo amapatsa zabwino zonse, angathenso kutsitsa munthu ku manda monga afunira. Tsopano mwana wanga, ukumbukire malangizo ameneŵa, asafafanizike mumtima mwako.

20“Tsopano ndikukudziŵitsa kuti Gabaele, mwana wa Gabriyasi, wa ku Ragesi, ku Mediya, ndidamsungiza ndalama zasiliva zoposa makilogramu 340.

211Tim. 6.6-8Usaope mwana wanga poona kuti tasanduka osauka. Uli kale ndi chuma chambiri ngati uwopa Mulungu ndi kulewa machimo, ndiponso ngati uchita zinthu zabwino pamaso pa Ambuye, Mulungu wako.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help