1Ndimalirira Chauta m'mavuto anga
kuti andiyankhe.
2Ndimati, “Pulumutseni, Inu Chauta,
kwa anthu onama ndi kwa anthu onyenga.”
3Mulungu adzakuchitani chiyani, anthu onyenganu?
Kodi adzakupatsani chilango cha mtundu wanji?
4Adzakuzunzani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo,
pamodzi ndi makala amoto a mtengo wa tsanya.
5Ndili ndi tsoka lalikulu,
chifukwa ndimakhala pakati pa anthu
onga mbuli za ku Meseki ndi Kedara.
6Ndakhala nthaŵi yaitali
pakati pa anthu odana ndi mtendere.
7Ine ndimafuna mtendere,
koma ndikalankhula za mtendere, iwo amafuna nkhondo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.