Yud. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akiyore aperekedwa kwa Aisraele

1Pamene phokoso la anthu ozungulira hema lija lidaleka, Holofernesi, mtsogoleri wamkulu wa ankhondo a Aasiriya, adalankhula ndi Akiyore ndi Amowabu onse pamaso pa magulu onse a ankhondo achilendo.

2Adati, “Ndiwe yani iwe Akiyore, ndinu yani inu aganyu a ku Efuremu, kuti nkumalosa zinthu pakati pathu, monga mwachitira leromu? Ndinu yani kuti mungatiletse kukamenya nkhondo ndi Aisraele? Mukuti Mulungu wao adzaŵateteza? Kodi pali mulungu wina woposa Nebukadinezara? Nebukadinezara adzatumiza gulu lake lankhondo kukapha Aisraele onse. Mulungu waoyo sangathe konse kuŵapulumutsa.

3Ife amene timatumikira Nebukadinezara, tidzaŵapha onse ngati ndi munthu mmodzi chabe. Sangathe kupambana mphamvu za ankhondo athu okwera pa akavalo.

4Tidzaŵatentha, ndipo mapiri ao adzanyowa ndi magazi ao, ndipo zigwa zao zidzadzaza ndi mitembo yao. Sadzatha kutichita kanthu, onsewo adzatheratu. Limeneli ndilo lamulo la mfumu Nebukadinezara, mbuye wa dziko lonse lapansi. Adalankhula ndipo mau ake sadzapita padera.

5“Koma iwe Akiyore, iwe Mwamoni waganyu chabe, mau amene walankhulaŵa lero ngaupandu. Kuyambira lero sudzandiwonanso mpaka nditalipsira gulu lonselo la anthu amene adathaŵa ku Ejipito.

6Tsono nditabwereranso, iweyo ankhondo anga adzakubaya m'nthiti mwako ndi lupanga ndi mkondo, choncho udzakhala mmodzi mwa ovulala.

7Tsopano anthu anga akutenga kupita nawe ku mapiri kukakusiya mu mzinda wina kumeneko.

8Koma sudzafa mpaka pamene anthu akumeneko adzaonongedwe onse.

9Ngati ukhulupirira kuti sitidzaŵagonjetsa, usaoneke wankhaŵa chonchi. Ndalankhula, ndipo mau anga sadzapita padera.”

Apita ndi Akiyore ku Betuliya

10Tsono Holofernesi adalamula anthu a m'hema mwake kuti agwire Akiyore, apite naye ku Betuliya, ndipo akampereke kwa Aisraele.

11Motero adamgwira namtulutsa m'hema nkupita naye ku chigwa. Kuchokera kumeneko adapita naye ku dziko lamapiri, mpaka adakafika ku akasupe a kunsi kwa Betuliya.

12Anthu amumzindamo ataŵaona, adatenga zida zao, natuluka mu mzinda kupita pamwamba pa phiri. Paphiripo onse oponya miyala adayamba kuŵaponya miyala adaniwo kuti asakwere.

13Koma Aasiriya adabisala m'munsi mwa phiri nakamangirira Akiyore ndi kumsiya patsinde pa phiri, iwowo nkubwerera kwa mbuye wao.

14Aisraele ena adatuluka mu mzinda natsikira kumene kunali Akiyore. Atammasula, adaloŵa naye mu mzinda nafika naye pamaso pa akuluakulu.

15Masiku amenewo akuluakuluwo anali aŵa: Uziya, mwana wa Mika wa fuko la Simeoni, Kabrisi mwana wa Gotoniele, ndi Karmisi mwana wa Melekiele.

16Akuluakuluwo adasonkhanitsa atsogoleri onse amumzindamo; anyamata ndi akazi onse adathamangira kumeneko. Adakhazika Akiyore pakati pa anthupo, kenaka Uziya adayamba kumfunsa zimene zidachitika.

17Iye poyankha adaŵauza zonse zimene zidachitika ku msonkhano wa Holofernesi, zimene iye adaanena pamaso pa atsogoleri ankhondo a Aasiriya, ndi za m'mene Holofernesi adaadzitukumulira pa zimene ankati aŵachite Aisraele.

18Anthuwo atamva zimenezi, adadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, ndipo adalira kwa Iye.

19Adati, “Inu Ambuye, Mulungu Wakumwamba, onani m'mene adani athu onyadaŵa apeputsira anthu anu. Mutimvere chifundo ndi kutithandiza.”

20Pambuyo pake adamtonthoza mtima Akiyore namuyamika chifukwa cha zonse zimene adachita.

21Msonkhano utatha, Uziya adatenga Akiyore kupita naye kwao, kumene adakonzera akuluakulu phwando. Usiku wonsewo adapemphera kwa Mulungu wa Israele kuti aŵathandize.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help