1 Gen. 46.8-27 Naŵa ana a Yakobe amene adapita ku Ejipito pamodzi ndi Yakobeyo ndi mabanja ao omwe:
2Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda,
3Isakara, Zebuloni, Benjamini,
4Dani, Nafutali, Gadi ndi Asere.
5Chiŵerengero chenicheni cha anthu obadwa mwa Yakobe chinali makumi asanu ndi aŵiri. Yosefe anali atakhazikika kale ku Ejipito.
6Tsono Yosefe adamwalira, abale ake ndi mbadwo wao wonse uja adamwaliranso.
7Ntc. 7.17 Koma adzukulu a Aisraele adabala ana ambirimbiri. Adachulukana nakhala amphamvu kwambiri nkudzaza dzikolo.
8 Ntc. 7.18 Pambuyo pake padaloŵa mfumu ina imene sidadziŵe za Yosefe.
9Mfumuyo idauza anthu ake kuti, “Aisraeleŵa akuchuluka kwambiri, ndipo ndi amphamvu kupambana ife.
10Ntc. 7.19 Mvetsani tsono, ife tichite nawo mwanzeru anthu ameneŵa. Tiŵachenjerere, kuti asachuluke, chifukwatu pa nthaŵi ya nkhondo, iwoŵa angathe kudzaphatikizana ndi adani athu, nadzalimbana nafe, kenaka nkudzachoka m'dziko mwathu muno.”
11Tsono adaika akapitao ao oŵagwiritsa mwankhanza ntchito yolimba Aisraelewo, kuti pakutero aŵafooketse. Aisraele adamangira Faraoyo mizinda ya Pitomu ndi Ramsesi, kumene Aejipito ankasunga chakudya chao.
12Koma Aisraele ankati akamaŵazunza kwambiri, ndi pamene iwo tsono ankachulukirachulukira, mpaka adabalalikira m'dziko lonselo. Motero Aejipito ankaŵaopa Aisraele,
13ndipo ankaŵakakamiza mwankhalwe kugwira ntchito yaukapolo.
14Moyo wa Aisraele unali woŵaŵa chifukwa cha ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, ndiponso ntchito zosiyanasiyana zam'minda. Ankaŵakakamiza mwankhanza kugwira ntchito zonse zolemetsa.
15Tsono mfumu ya ku Ejipito ija idaitana azamba amene ankathandiza azimai achihebri pochira. Wina mwa azamba ameneŵa anali Sifira, wina anali Puwa. Mfumuyo idauza azambawo kuti,
16“Mukamathandiza azimai achihebri pochira, akabadwa mwana wamwamuna, mupheni, akakhala wamkazi, mlekeni.”
17Koma azambawo ankaopa Mulungu, kotero kuti mau a mfumu aja sadaŵasamale konse, ana aamunawo ankangoŵaleka amoyo.
18Tsono mfumu ija idaŵaitana azamba aja niŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵaleka ana aamuna osaŵapha?”
19Azamba aja adayankha kuti “Azimai achihebri safanafana ndi azimai achiejipito. Iwo ngamphamvu, amati mzamba asanafike, mwana amakhala atabadwa kale.”
20Choncho Mulungu adaŵakomera mtima azambawo, mwakuti Aisraele adapitirirabe kuchulukana, nakhala amphamvu kwambiri.
21Tsono chifukwa choti azambawo ankaopa Mulungu, Mulungu adaŵapatsa mabanja.
22Ntc. 7.19 Pamenepo Farao adalamula anthu ake kuti, “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa mwa Ahebri azimponya mu mtsinje wa Nailo, koma ana onse aakazi aziŵaleka, azikhala moyo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.