Hag. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Lamulo la kumanganso Nyumba ya Mulungu

1 Eza. 4.24—5.2; 6.14 Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga. Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndiponso kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, udati,

2“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Anthu aŵa amanena kuti, ‘Nthaŵi siinafike yoti nkumanganso Nyumba ya Chauta.’ ”

3Tsono Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti:

4“Kodi nzabwino zimenezi kuti inuyo muzikhala m'nyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ili bwinja?

5“Nchifukwa chake tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti muganizepo bwinotu pamenepa.

6Mwafesa zambiri, koma mwakolola pang'ono. Mumadya, koma osakhuta. Mumamwa, koma ludzu osatha. Mumavala, koma osamva kufunda. Malipiro a anthu antchito ndi osakwanira mpang'ono pomwe,

7“Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti muganizeponso bwinotu pamenepa.

8Kwerani ku mapiri, mukadule nsichi, mudzandimangire Nyumba yoyenera, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiriramo ulemerero.

9“Mwakhala mukuyembekeza zokolola zambiri, koma mwangopeza pang'ono. Pamene munkatuta zokolola zanu, Ine ndidangozimwazamwaza. Tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, Ndidachitiranji zimenezi? Chifukwa chake nchakuti Nyumba yanga ndi bwinja, pamene aliyense akutanganidwa nkumanga nyumba yake.

10Nkuwonatu mvula yati zii, nthaka yati gwa.

11Nkuwonanso ndagwetsa chilala pa dziko lonse, pa minda ya tirigu, ya mphesa ndi ya mitengo ya olivi, pa zonse zomera pa nthaka, ndi pa zonse zimene anthu amalima, ndiponso pa anthu ndi nyama zomwe.”

Anthu amvera lamulo la Chauta

12Pamenepo Zerubabele mwana wa Salatiyele, Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe, ndi anthu ena onse obwerako ku ukapolo, adachita zimene Chauta Mulungu wao adanena. Adamva mau a mneneri Hagai amene Chauta adamtuma, ndipo adachita mantha kwambiri.

13Motero Hagai, wamthenga uja, adaŵauza mau a Chauta akuti, “Ine Chauta ndikukuuzani kuti ndili nanu ndithu.”

14Tsono Chauta adalimbitsa mtima Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse. Adabwera, nayamba kugwira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wao,

15pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiŵiri pamene Dariusi anali mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help