1 Lk. 5.1-3 Yesu adayambanso kuphunzitsa pambali pa Nyanja ya Galileya. Anthu ochuluka adasonkhana kumeneko, kotero kuti Iye adaayenera kuloŵa m'chombo, nakhala pansi m'menemo panyanjapo. Anthu onse adaakhala pansi pa mtunda m'mphepete mwa nyanjayo,
2ndipo Yesu adayamba kuŵaphunzitsa zambiri m'mafanizo. Poŵaphunzitsa adati,
3“Mvetsetsani! Munthu wina adapita kukafesa mbeu.
4Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola.
5Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga, chifukwa nthakayo inali yosazama.
6Koma pamene dzuŵa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu.
7Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija, kotero kuti mbeuzo sizidabereke konse.
8Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidamera bwino nkukula, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi khumi.”
9Tsono Yesu adati, “Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”
Za cholinga cha mafanizo(Mt. 13.10-17; Lk. 8.9-10)10Pamene Yesu anali payekha, ophunzira khumi ndi aŵiri aja pamodzi ndi enanso amene ankakhala naye adadzamufunsa za mafanizowo.
11Iye adaŵayankha kuti, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amene ali kunja, zonse amazimvera m'mafanizo chabe,
12Yes. 6.9, 10 kuti choncho, monga mau a Mulungu aja amanena,
“ ‘Kuyang'ana ayang'ane ndithu,
koma asapenye kanthu,
ndipo kumva amve ndithu,
koma asamvetse kanthu,
kuti angatembenuke mtima,
ndipo Mulungu angaŵakhululukire.’ ”
Tanthauzo la fanizo la wofesa mbeu(Mt. 13.18-23; Lk. 8.11-15)13Pambuyo pake Yesu adaŵafunsa kuti, “Monga simukulimvetsadi fanizo limeneli? Nanga mudzamvetsa bwanji fanizo lina lililonse?
14Wofesa mbeu uja ndi amene amafesa mau a Mulungu.
15Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma nthaŵi yomweyo Satana amabwera, nkuchotsa mau aja amene adafesedwa m'mitima mwao.
16Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe.
17Tsono popeza kuti mauwo sadazike mizu yozama, anthuwo amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo anthuwo amabwerera m'mbuyo.
18Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu.
19Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.
20Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amamva mau a Mulungu, naŵalandira. Anthu otere amabereka zipatso, mwina makumi atatu, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi khumi.”
Za nyale yovundikira ndi mbiya(Lk. 8.16-18)21 Mt. 5.15; Lk. 11.33 Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amatenga nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi? Suja amaiika pa malo oonekera?
22Mt. 10.26; Lk. 12.2Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzaonekera poyera.
23Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”
24 Mt. 7.2; Lk. 6.38 Adaŵauzanso kuti, “Muzisamala pa mau amene mumamva. Muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu, ndipo inuyo adzakubzoletserani.
25Mt. 13.12; 25.29; Lk. 19.26Paja amene ali ndi kanthu kale, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.”
Fanizo la mbeu zimene zimamera ndi kukula26Yesu adaŵauzanso kuti, “Za Ufumu wa Mulungu tingazifanizire motere: munthu afesa mbeu m'munda.
27Iyeyo atha kumangogona usiku, m'maŵa nadzuka, nthaŵi yonseyo mbeu adafesa zija zikumera ndi kukula, mwiniwakeyo osadziŵa m'mene zonsezi zikuchitikira.
28Paja nthaka imabereketsa mbeuzo yokhayokha. Umayamba ndi mmera, kenaka ngala, pambuyo pake njere m'ngala muja zimakhwima.
29Yow. 3.13Tsono mbeuzo zikacha, munthu uja amatenga mpeni wodulira, pakuti nyengo yokolola yafika.”
Fanizo la njere ya mpiru(Mt. 13.31-32, 34; Lk. 13.18-19)30Yesu adatinso, “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani? Kaya tiwufanizire ndi chiyani?
31Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru. Pamene aifesa m'nthaka, ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina pansi pano.
32Koma akaifesa, imamera, mbeu yake nkukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse. Imachita nthambi zazikulu, kotero kuti mbalame zimatha kudzamanga zisa mumthunzi mwake.”
33Yesu ankaphunzitsa anthu ndi mafanizo ambiri onga ameneŵa, polinganiza ndi nzeru za anthuwo.
34Sankaŵaphunzitsa popanda mafanizo. Koma ankati akakhala payekha ndi ophunzira ake, ankaŵatanthauzira zonse.
Yesu athetsa namondwe(Mt. 8.23-27; Lk. 8.22-25)35Tsiku lomwelo, dzuŵa litaloŵa, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya.”
36Tsono iwo adasiya khamu la anthu lija, natenga Yesu m'chombo momwe adaalimo. Padaalinso zombo zina zotsagana naye.
37Tsono padauka namondwe woopsa. Mafunde ankaloŵa m'chombomo, kotero kuti chidaayamba kudzaza ndi madzi.
38Koma nthaŵi imeneyo Yesu anali kumbuyo m'chombomo, ali m'tulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?”
39Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “Tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu.
40Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha? Kani mulibe chikhulupiriro inu?”
41Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “Kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.