1
6Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya.
7Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala.
8Madzulo dzuŵa litapepa, aŵiriwo adamva mtswatswa, Chauta akuyenda m'mundamo, ndipo iwo adabisala m'katikati mwa mitengo, kuti Iye angaŵaone.
9Koma Chauta adamuitana Adamu uja kuti, “Kodi uli kuti?”
10Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m'mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.”
11Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? Kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?”
12Pamenepo Adamu adayankha kuti, “Mkazi mudandipatsayu ndiye amene anandipatsa zipatsozo kuti ndidye, ndipo ndadyadi.”
13 adatcha mkazi wake Heva, chifukwa choti iyeyu anali mai wa anthu onse.
21Ndipo Chauta adasokera Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa naŵaveka onse aŵiriwo.
Adamu ndi Heva atulutsidwa m'munda22 Chiv. 22.14 Chauta adati, “Tsopano munthuyu wakhala monga tiliri ife, popeza kuti akudziŵa zabwino ndi zoipa. Asaloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyowo ndi kukhala moyo mpaka muyaya.”
23Motero Chauta adamtulutsamo m'munda mwa Edeni muja, kuti azilima m'nthaka momwe adachokera.
24Atampirikitsira kunja Adamuyo, Mulungu adaika akerubi kuvuma kwa munda wa Edeni. Adaikanso lupanga lamoto limene linkazungulira mbali zonse, kutchinjiriza mtengo wopatsa moyo uja, kuti wina asaufike pafupi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.